0% found this document useful (0 votes)
563 views50 pages

Chichewa Literature

Uploaded by

phedulosacranie
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as DOCX, PDF, TXT or read online on Scribd
0% found this document useful (0 votes)
563 views50 pages

Chichewa Literature

Uploaded by

phedulosacranie
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as DOCX, PDF, TXT or read online on Scribd
You are on page 1/ 50

KWALIMBA UTA NDI NTHANO ZINA

Mlembi: Dyson Gilbert Gonthi


Mtundu wankhani: Nthano Zopeka
Zolinga Za mlembi
 Kuthandiza achinyamata kuti akhale ndi chikhalidwe chabwino munjira zawo zatsiku ndi tsiku.
 Kuunikira achinyamata kuti athe kupeza njira zothetsera mavuto amene angakumane nawo pamoyo.
 Kulimbikitsa achinyamata kuti akhale ndi ntima wodzikhulupirira iwo eni.

Kumbutso: Nthano zimayimbidwa kudzera kunyama zosiyanasiyana kuphatikizapo ziweto. Nyamazi zimagwiritsidwa ntchito molingana
ndi makhalidwe ake. Makhalidwe ndi maonekedwe anyamazo ndiwo amafananitsidwa ndi makhalidwe a anthu.

Mutu I: Za Chuma
Atengambali/ampangankhani: Chingaipe
: Mphunzitsi
: Bwatamu; m’modzi mwa ana aja
: Ana
Malo Ochitikira Nkhani: m’mudzi wina m’malire a nkhalango ya M’ndirasadza
: Kusukulu

Kusanthula nkhani yonse


Mchezo wa Chingaipe ndi ana
 Mwana wina adafunsa Chingaipe momwe makolo amayendetsera malonda awo azungu asadabwere popeza adamva kuti panthawiyi
kudalibe ndalama.
 Chingaipe adafotokozera mwanayu ndi anzakewo kuti ndalama kudalibedi mwakuti makolo ankangosinthana zinthu. Mwachitsanzo,
ngati munthu akufuna mbiya yophikamo zakudya koma iye ali ndi mafuta amsatsi, amasinthanitsa mafuta akewo ndi mbiyayo.
 Malonda amayeza ndi maso; akakhutira amasinthana malingana ndi m’mene zinthuzo zikuonekera.
 Asing’anga akachiritsa munthu amamulipiritsa molingana ndi kukula kwa matenda akewo.

Kuipa kwa malonda osinthanitsa


 Adalibe muyeso wachilungamo; adali ngati wachiona ndani.
 Anthu ankangokhutira ndi zomwe apeza.
 Amafuna munthu olimbikira ntchito; amene adalibe chilichonse choti n’kusinthanitsa ndi chinzake amavutika kuti akhale ndi kanthu.

Ubwino wogulitsa katundu wosinthanitsa ndi ndalama


 Anthu amaona chiwerengero chandalama ndi katundu akugulitsidwayo.
 Zimakhala kwa wogulitsayo kukhutitsidwa choncho sipakhala zoberana.

Page 1
Kumbutso: Azungu atabwera ku Afrika adapitirizabe malonda osinthanitsa ndipo ankachita malonda osinthanitsa minyanga yanjovu ndi
nsalu, mfuti ndi anthu kenako adabweretsa malonda osinthanitsa zinthu ndi makobidi. Azungu ankachitanso malonda ogulitsa anthu omwe
amakakhala akapolo ndipo amakawagulitsa kumaiko akutsidya la nyanja.

Malangizo a Chingaipe kwa achinyamata amene adatsiriza sukulu ndipo ankangokhala.


 Ntchito ndi kuganiza kwamunthu pa zimene angachite pamoyo wake: osamangodalira kuti udzalembedwe ntchito mukamaliza
maphunziro.
 Sukulu ndi mfungulo chabe; imangochangamutsa munthu. Cholinga chamaphunziro ndicho kuthandiza anthu kuti azitha kuchita zinthu
paokha zoti akhoza kumagulitsa osati kupereka maganizo kwa anthu oti akatsiriza sukulu akalowa ntchito yakuofesi.
 Atha kuchita ntchito yosamala zachilengedwe monga kuweta njuchi, kufutsa ndiwo zamasamba, kukonza zinthu zochokera
kuphwetekere, kuweta nkhanga komanso kugulitsa zipatso zamtchire.
 Zinthu zotsatirazi zingathe kutukula dziko la Malawi pachuma:
 Kutsatira masomphenya a malemu Bingu Wa Mutharika oti, “Dziko la Malawi silosauka poti lili ndi china chilichonse chothandiza
pachitukuko koma umphawi uli ndi anthu omwe safuna kudzipereka pogwira ntchito. M’mawuwa akutanthauza izi:
 Miyala yamtengo wapatali yomwe mayiko akunja amaifuna kwambiri imene amapangira mphete, mikanda, laimu, fetereza ndi
zinthu zina zambiri.
 Madzi a m’nyanja ya Malawi komanso mitsinje: kuchita ulimi wamthirira (ulimi wangalande) komanso kuwasunga m’maiwe
nkumawetamo nsomba komanso kumamwetsera ziweto.
 Luso lapadera pambewu zomwe timalima monga mpunga: mpunga titha kumapangira ice cream, mowa komanso chingwa (bread).
Mbewu zina monga chimanga ndi tirigu zilinso ndi ntchito zina.
 Boma lipereke mpata kwa anthu ena kuti adzayambitse makampani mosayang’anira kuti kampani ngati zomwezo zilipo kale.
 Kutsatira malamulo azokopa alendo posamala zachilengedwe monga nyama, mapiri, mitsinje, nkhalango ndi zina zambiri.

Maganizo a Chingaipe poomba mkota


 Palibe chifukwa chomakhalira ndi njala komanso pa umphawi popeza dziko la Malawi ili ndi madzi ochuluka komanso nthaka
yachonde.
 Vuto la Amalawi ndi kusakonda kugwira ntchito limodzi: aliyense amafuna kugwira ntchito payekha.
 Amalawi amakonda kugona maola ambiri m’malo mogona maola ochepa n’kupitanso kukagwira ntchito usiku monga amachitira
anzathu akunja.

Azungu ndi anthu akuda


 Azungu:
 Safuna anthu akuda azitukuka.
 Amapondereza anthu akuda m’njira zambiri.
 Amasowetsa mtendere anthu akuda m’maiko monga Jamaica, Amerika ndi Mangalande
 Safuna anthu akuda azikhala ozindikira n’cholinga choti aziwapondereza.
 Ndi odzikonda ndipo safuna kuyamikira zochita zamunthu wakuda.

Page 2
 Amati munthu wakuda sangachite chinthu chodalirika; zochita zamunthu wachikuda ndi zachikunja.
 Amati iwo amachita zodalirika komanso zofunika.
 Amadziwa kuti anthu akuda ndi olimbika komanso anzeru mwakuti atha kuwapitirira n’chifukwa chake amafuna
kuwapondereza kuti iwo azikhalabe pamwamba nkumawalamulira pantchito.
 Amafuna anthu akuda asiye miyambo yawo nkutenegera khalidwe lachizungulo chonsecho zochita zawo n’zopanda pake,
zolaula komanso zosagwirizana ndi chikhalidwe cha anthu akuda.
Adachenjera potizindikiritsa za sukulu nkutibisira kuti nzeru zamaphunziro timachitazo zitha kutithandiza kuti tizichita zinthu patokha.
Akationa kuti munthu wakuda wayamba kuzindikira amamukankhira kukayamba ntchito mmalo moti agwiritse ntchito nzeruzo pa ulimi
wabwino( kuwerengera zogwiritsa ntchito pa ulimiwo komanso kudziwa phindu lambewuzo)
 Amati anthu akuda si anthu koma nyama zakutchire choncho adalengedwa kuti azithandiza azungu.
 Anthu akuda:
 Ankaona azungu ngati mizimu choncho kudali kovuta kuwatsutsa.
 Ankati dziko ndi la azungu popeza katundu yemwe ankagwiritsidwa ntchito anali wochokera kwa azungu monga ku Ulaya.
 Ankaganiza kuti katundu wawo ngakhalenso zovala zawo sizabwino komanso zawamba.
 Ankatamandira anzawo omwe amavala zovala zakunja.

Zomwe zimabweza chitukuko pambuyo ku Malawi.


 Kukhulupirira zachizungu kwambiri.
 Malipiro ochepa omwe anthu amalandira.
 Kusalola kukhala ndi mpikisano wantchito zikuluzikulu zofunika za makampani. Mwachitsanzo, ku Malawi tili ndi vuto lamagetsi
kamba kakuti kampani ndi imodzi. Pakanakhala kampani ena opikisana nayo bwenzi anthu akusankha kampani yomwe
ikuwasangalatsa. Eni kampani omwe sali pampikisano ndi makampani ena amatayirira pakagwiridwe ka ntchito zawo ndipo sadandaula
popeza ali wokha.

Mfundo zazikulu m’nkhaniyi


 Kudzikonda kwa azungu
 Safuna anthu akuda azitukuka.
 Safuna anthu akuda azikhaLa ozindikira n’cholinga choti aziwapondereza.
 Safuna kuyamikira zochita zamunthu wakuda.
 Amati munthu wakuda sangachite chinthu chodalirika; zochita zamunthu wachikuda ndi zachikunja.
 Amati iwo amachita zodalirika komanso zofunika.
 Amafuna anthu akuda asiye miyambo yawo nkutenegera khalidwe lachizungulo chonsecho zochita zawo n’zopanda pake,
zolaula komanso zosagwirizana ndi chikhalidwe cha anthu akuda.
 Kusadziwa kwa anthu akuda
 Ankaona azungu ngati mizimu choncho kudali kovuta kuwatsutsa.
 Makolo ankati dziko ndi la azungu popeza katundu yemwe ankagwiritsidwa ntchito anali wochokera kwa azungu monga ku
Ulaya.
 Ankaganiza kuti katundu wawo ngakhalenso zovala zawo sizabwino ndi zawamba.

Page 3
 Ankatamandira anzawo omwe amavala zovala zakunja.
 Kupondereza
 Azungu safuna anthu akuda azikhala ozindikira n’cholinga choti aziwapondereza.
 Azungu amadziwa kuti anthu akuda ndi olimbika komanso anzeru mwakuti atha kuwapitirira n’chifukwa chake amafuna
kuwapondereza kuti iwo azikhalabe pamwamba nkumawalamulira ndi pantchito
 Kusakondana kwa anthu akuda
 Kusagwirizana ndikuchitirana nsanje pa ntchito za malonda.
 .Kusalolera makampani ena awiri kapena atatu kugwira ntchito imodzi kuti pakhale kupkisana.
 .Kusakhudzidwa ndi mavuto a anzawo: Kulemba ana anzawo komanso anthu ndikumawapatsa malipiro ochepa m’maesiteti.

Maphunziro kapena uthenga m’nkhaniyi


 Anthu ena safunira anzawo zabwino.
Azungu safunira anthu akuda zabwino.
 Safuna anthu akuda azitukuka.
 Safuna anthu akuda azikhala ozindikira n’cholinga choti aziwapondereza.
 Safuna kuyamikira zochita zamunthu wakuda.

Matanthauzo amawu ena
 Adziwe mfolo :achenjere
 Akungotha gaga :angokhala nkumadya basi
 Ogunata :opusa/opepera
 Zinthu zakampeni kumphasa :zosungirana mangawa
 Atchera kumwezi nkhanga zaona :aonekera poyera
 Mwamvu :nthawi ya chirimwe
 Kuphimba m’maso :kupusitsa
 Kutengera kuntoso ngati nyama ya galu :kunyozedwa
 Wamvula za zakale :munthu wachikulire

 Anthu akuMalawi amakanika kutukula dziko chonsecho zoyenereza ali nazo ndithu.
Anthu aku Malawi atha:
 Kutsatira masomphenya a malemu Bingu Wa Mutharika oti, “Dziko la Malawi silosauka poti lili ndi china chilichonse
chothandiza pachitukuko koma umphawi uli ndi anthu omwe safuna kudzipereka pogwira ntchito.
 Kuchita ulimi wamthirira (ulimi wangalande) pogwiritsa ntchito nyanja komanso mitsinje yomwe ilipo m’dziko mwawo.
 Kusamala zachilengedwe n’kumatsata malamulo azokopa alendo.
 Kudzipezera chochita m’malo modikira kulembedwa ntchito yakuofesi.
 Kugwiritsa nzeru zozama zomwe aphunzira kusukulu za ukachenjede pantchito yodzilemba okha.

Page 4
Mutu II: HIV/AIDS
Nthano mwachidule
HIV ndi kachilombo kamene kamayambitsa kutha kwa chitetezo chachibadwidwe mnthupi lamunthu. Ena amati kachilomboka kadachita
kupangidwa ndi akatswiri aza sayansi,ena amati kadachokera kunyama ziweto nkhosa ndi ng’ombe,enanso amati munthu ndi nyani
wochedwa chimpazi izi zikusonyeza kuti sikadziwika bwino komwe kadayambira. Kali ndi zizindikiro kakalowa m’thupi mwamunthu
komanso nkopeweka. Kuno kuMalawi anthu adakatulukira mzaka za 1985 komabe kadali katayamba kale.

Zomwe zimachitika kachilombo ka HIV kakapezeka mnthupi lamunthu


 Chitetezo chimachepa
 Thupi limakhala lopanda mphamvu
 Munthu akadwala matenda aliwonse kumakhala kovuta kuti achire.

HIV idadziwika ku Malawi nanga anthu anali ndi maganizo anji panthawiyi
 Panthawiyi anthu anali asadatulukire, ankangoti ndi matenda akanyera/kunyentchera moti amataya nthawi nkumapita kwa asing’anga
mpaka ankafa nawo.
 Ena ankangoganizirana za ufiti kapena kulodzana pantchito, pabizinesi, paudindo kumpingo kapena kulimbanirana ufumu.

Komwe idayambira komanso komwe idachokera HIV/AIDS


 Ena amati idayambira ku Amerika, ku Kenya komanso ku Australia kotero nkovuta kudziwa kwenikweni komwe idayambira.
 Amati akatswiri odziwa za chirengedwe chathupi lamunthu ku Amerika ndiwo adayambitsa mliriwu.
 Ena amati akatswiri aku Amerika adakapanga kuchokera ku kachirombo kam’nthupi lankhosa(bira/mberere) n’kuphatikiza ndi
kachirombo kam’nthupi lang’ombe.
 Ena amati kadayambika ndi munthu wina yemwe ankachita zolaula ndi chinyama chokhala ngati nkhwere/nyani ndipo adayamba
kuonetsa zizindikiro zoti m’nthupi lake muli kachirombo koononga chitetezo chachilengedwe m’nthupi.

Zizindikiro za HIV/AIDS
 Kutsekula m’mimba kawirikawiri
 Kunyozoloka kwa tsitsi ngati bweya
 Lilime limaoneka lambuu
 Kutsokomola pafupipafupi
 Kulefuka ndi kuchita thukuta nthawi iliyonse
 Kuonda ndi kusanza
 Mashingozi

Njira zotengera HIV

Page 5
 Kukhudza magazi amunthu yemwe ali ndi kachilomboka
 Kubwerekana malezala
 Kugwiritsa ntchito jakisoni m’modzi anthu ambiri
 Kugonana ndi akazi kapena amuna ochuluka/ambirimbiri
 Pobereka kapena kuyamwitsa amayi atha kumpatsira mwana

Mtundu wina wa HIV


 Kachilomboka kadzafala ngati mphepo ndikumaoneka mitundumitundu monga momwe imaonekera nthenda ya khansa.

Kapewedwe ka HIV/AIDS
 Kupewa mchitidwe wachiwerewere
 Kukhulupirirana m’banja
 Kugwiritsa ntchito makondomu kwa iwo amene sanakwatirane koma sangathe kupirira
 Amayi aleke kubereka ngati adziwa kuti ali ndi HIV.

Kumbutso:
 Aliyense aziyesetsa kusamalira thupi lake potsatira malangizo a zaumoyo.
 Munthu ayenera kukayezetsa magazi kuti adziwe m’mene m’nthupi mwake muliri.
 Phukusi lamoyo sakusungira ndi mnzako, umasunga wekha.
 Pachina chilichonse pamakambidwa za HIV/AIDS popeza chilichonse gwero lake ndi moyo wathanzi.

Mfundo zazikulu m’nkhaniyi


 Kusasamala moyo wa ena:
 . Akatswiri adakonza mwadala kachirombo ka HIV kamene kakuononga moyo wa anthu ena
padziko lapansi.
. Munthu wina ankachita zolaula ndi nyama mpaka adatenga HIV.
 Kusadziwa:
 .Anthu posadziwa HIV/AIDS ku Malawi, ankayesa kuti ndi nthenda ya Kanyera kapenanso kuti anthu akulodzana
pamaudindo kumpingo ndi kuofesi.
Tipewe chiwerewere
Anthu ambiri adamwalira chifukwa cha kugonana ndi akazi kapena amuna ambiri.
Tikayezetse magazi
Ndibwino kuyezetsa HIV kuti udziwe m’mene mnthupi mwako muliri.

 HIV/AIDS ndi yopeweka.


Pali njira zambiri zopewera HIV/AIDS monga kukhulupirika m’banja, kugwiritsa ntchito makondomu ndi kudziletsa.

Page 6
Maphunziro m’nkhaniyi
 Anthu adaonongeka chifukwa cha kusadziwa.
Anthu posadziwa HIV/AIDS ku Malawi, ankayesa kuti ndi nthenda ya Kanyera kapenanso kuti anthu akulodzana
pamaudindo kumpingo ndi kuofesi mwakuti anthu ambiri amapita kwa asing’anga ndipo adamwalira.

Mutu III: Malangizo a Nkhanu


Nthano mwachidule
 Njoka inali kudya ana a apumbwa pamene makolo awo apita kukasaka zakudya. Apumbwawo ankadandaula nkumalira mpaka Nkhanu
idamva kulirako. Apumbwa adapempha Nkhanu kuti iwathandize ndipo Nkhanuyo idapeza njira yoika nsomba m’njira yomwe njoka
imayendamo mpaka ku mphako komwe inkabisala. Nkhanu idati Sisinya zidzatsatira fungo lansomba mpaka zidzapha njokayo. Sisinya
zidapha mbalame zonse mumtengomo.

 Atengambali m’nkhaniyi
 Nkhanu
 Mbalame wa mtundu wa pumbwa
 Njoka

Malo ochitikira nkhani:


a) Mumtengo waMkuyu
 Mumamakhala a pumbwa komanso njoka yomwe imadya ana a mbalame asanaphukire ndi ubweya omwe.

b) Kumtsinje
 Komwe nkhanu inkakhala ndipo idamva chisoni ndi kulira kwa mbalame. Nkhanuyo idacheza ndi mbalame pamalopa, idamva
madandaulo ake ndipo idalonjeza kuthetsa vuto la mbalame.

Kuchenjera kwa njoka


 Imadya ana a mbalame panthawi imene mbalame zikuluzikuluzo zapita kukafuna zakudya.

Kupusa kwa apumbwa


 Sadaganizire zomwe zikadatha kuchitika kwa ana awo pamene iwo amanyamuka kukafuna zakudya.
 Amadziwa kuti njoka ikutha ana awo koma palibe chomwe adachita kuti njokayo isiye khalidweli, ankangodandaula komanso
ankangolira.

Page 7
Njira yomwe nkhanu idakonza yophera njoka
 Idauza Apumbwa kuti itenga nsomba ndikuika m’njira yomwe njoka imadutsa pokalowa kumphako komwe imakhala.
 Idati Sisinya ndi zomwe zidzalondole njoka ndikukaipha kumphako komweko.
 Njirayi sidali yabwino popeza Sisinya zidapha mbalame zonse mumtengomo.

Mfundo zazikulu m’nkhaniyi


 Kuthandiza :Nkhanu idathandiza mbalame kuti zithane ndi njoka yomwe inkadya ana awo.
 Chikondi :Nkhanu idasonyeza chikondi kwa mbalame pomvetsera madandaulo ake ndi kupeza njira yothandiza pa zimene
mbalame zimadandaula.
 Kusakhulupirirka:Sisinya sizidakhulupirike popeza m’malo mopha njoka zidapha mbalame zonse mumtengo wamkuyu.
 Kuchenjera :Njoka imadya ana a mbalame panthawi imene mbalame zikuluzikuluzo zapita kukafuna zakudya.
 Kudalira :Mbalame zidadalira Nkhanu kuti iwathandiza pothana ndi Njoka yomwe imawadyera ana. Nkhanu idadalira
Sisinya kuti zidzalondola Njoka mpaka kukaipha kumphako komwe inkakhala.

Maphunziro m’nkhaniyi
 Ndi bwino kusamala ndi omwe tikufuna kuti atithandize pamene takumana ndi vuto.
Nkhanu idauza Sisinya kuti ithandize kupha Njoka popeza idaona kuti Sisinya ndi zomwe zingathe kupha Njokayo. Sisinyazo,
m’malo mwake, zidapha mbalame zonse mumtengo wamkuyu.

Chamwini nchamwini
Tidziganizanso mozama pamalangizo omwe tapatsidwa kuti tiwatsatire.Pumbwa adadalira kwambiri nzeru za ena koma
sizinamuthandize.

Mutu IV: Malodza a Khungubwe


Nthano mwachidule
Khungubwe anali ndi chisa muntengo wina. Tsiku lina, m’Juni kukuzizira zedi, adawona Gweyani atazizidwa ndipo atasowa koti nkubisala.
Gweyaniyo adali patsinde pamtengo womwe Khungubwe adamanga chisa chake. Khungubwe adamva chisoni ataona m’mene Gweyani
adazizidwira ndi chisanu ndipo adadandaulira Gweyaniyo. Gweyani adauza Khungubwe kuti asavutike ndikumdandaulira iye; angotaya
nthawi. Gweyani adayankhula nati Khungubweyo adangofuna kuchita matama kuti awonetse kuti ali pabwino. Pamene Khungubwe
adapitiriza kumvera chisoni Gweyani, Gweyani adayankha mwaukali nati Khungubweyo achite zake. Khungubwe atapitiriza kulangiza
Gweyani, Gweyaniyo adangokwera mumtengomo nkukasulakasula chisa cha Khungubweyo.

Kusanthula nthano yonse


Page 8
Atengambali
 Khungubwe
 Gwenyani

Malo ochitikira nkhani


Mumtengo : Khungubwe adamangamo chisa chake.
Patsinde lamtengo : Gweyani adayimapo atazizidwa ndipo adaonedwa ndi Khungubwe
Mchisa : Chisa chomwe chidamangidwa ndi nkhungubwe kuti adzikhalamo.

Mfundo zazikulu m’nthanoyi


 Chisoni ndi chikondi
 Adamvera chisoni Gweyani popeza adali atazizidwa.
 Adalangiza Gweyani kuti adzimangire pokhala.

 Mwano
 Gweyani adayankha Khungubwe kuti asavutike ndikumumvera chisoni; angotaya nthawi.
 Gweyani adayankha mwaukali pamene Khungubwe ankamumvera chisoni kuti adazizidwa.
 Gweyani adauza Khungubwe kuti ntchito yake n’kukamba za anthu ena basi.
 Adamfunsa Khungubwe kuti anene chomwe anali kudziyesa.

 Kuganiza molakwika
 Gweyani atamva kuti Khungubwe ali kumumvera chisoni adaganiza kuti Khungubweyo angofuna kuonetsa kuti iye adali pobisala
pabwino ndipo ankangofuna kuchita matama.

 Nkhanza
Gweyani adakwera mumtengo n’kukakasulakasula chisa cha Khungubwe.
 Ulesi
Gweyani akuonetsa kuti ndi kanyama kaulesi polephera kudzimangira yekha chisa choti adzikhalamo pa nthawi yozizira kapena
yotentha.
 Kusadzidalira
Gweyani adali nyama yosadzidalira, imazizidwa ndi chisanu koma simadzimangira yokha pokhala.

Maphunziro
 Chisoni chimaphetsa

Page 9
 Khungubwe adachitira chisoni Gweyani atazizidwa namulangiza kuti adzimangire pokhala. Gweyani adayankha mwamwano
komanso mwaukali kuti Khungubweyo achite zake ndipo pamene Khungubwe adapitiriza kulangiza Gweyani adamusasulira chisa.

 Ena akavutika safuna kuthandizidwa kamba koganiza molakwika


 Gweyani atazizidwa sadafune kuti Khungubwe amuthandize popeza ankaganiza kuti Khungubwe akuchita matama kuti aoneke kuti
ali pabwino.

Mutu V: Udani wa Katundulu ndi Njovu


Nkhani Mwachidule
Njovu sidali kupeza bwino tsiku lina idakhala patsinde la mtengo wina osadziwa kuti mumtengomo mudali chisa cha Katundulu.
Mwatsoka chitamba cha njovuyo chidatsotsola chisacho ndipo ana a Katundulu adagwa nkufera pomwepo. Atafika akatundulu adaona
ana akufawo ndipo patsikuli chidani chidayambika. Katundulu wamkazi adali kudandaula nthawi zonse. Mpheta, bwenzi la Katundulu
wamkazi adafunsa mzakeyo chomwe ankalirira nthawi zonse. Katundulu atafotokoza zomwe idachita njovu, Mpheta idaumuuza kuti
adayenera kuyipha njovuyo. Chule ndi yemwe adapereka njira yophera njovu: adakhala pafupi ndi dzenje lalikulu nkumalira ndipo
njovu idagwera m’dzenjemo pamene idalondola komwe kunali chuleko poganiza kuti kudali madzi popeza inkakhulupirira kuti chule
salira popanda madzi.

Kusanthula nthano yonse


 Ategambali
.Katundulu
.Njovu
.Chule
.Mpheta
 .

Malo ochitikira nkhani


 Mumtengo : Akalitundulu anali kukhalamo ndipo mudali chisa ana awo.
 Patsinde pa mtengo : Njovu idakhalapo isakupeza bwino ndipo mwatsoka idasasula chisa cha
akatundulu mwakuti ana awo adagwa nkufa pomwepo.
 Padzenje :Chule ankalira ndipo njovu idagwera pamene inkayesa kuti pali madzi pokhulupirira kuti chule salira
popanda madzi.
Kusiyana kwa Katundulu wamkazi ndi wamamuna
Katundulu wamkazi adadandaula kwambiri kamba ka imfa ya ana ake mwakuti adapitiriza kudandaula nthawi zonse mpaka mpheta

Page 10
idafunsa chomwe chimachititsa Katunduluyo kuti azidandaula chotero.

Maganizo oyipa ampheta


Mpheta idapereka malangizo oyipa kwa Katundulu wamkazi oti njovu idayenera kuphedwa. Njovu sidayenere kuphedwa popeza
sidachitire dala kupha ana a Katundulu
Mfundo zazikulu
 Kusunga chidani: Katundulu atazindikira kuti ana ake adafa chifukwa choti njovu idasasula chisa, adasungira njovuyo
mangawa ndipo pamapeto pake adayipha.

 Kusazindikira:Njovu sidazindikire kuti pamane chule ankalirapo apadali dzenje lalikulu. Iyo idangokhulupirira kuti
pakulira chulepo pali madzi popeza chule salira popanda madzi.

 Kupereka malangizo oyipa: Mpheta idapereka malangizo oyipa kwa Katundulu wamkazi
oti njovu idayenera kuphedwa. Njovu sidayenere kuphedwa
popeza sidachitire dala kupha ana a Katundulu.

 Kudalira: Katundulu adadalira mpheta yomwe idapereka ganizo loti njovu iphedwe ndipo
adadaliranso chule yemwe adakonza njira yophera njovu.

 Kuganiza mwakuya: Chule adaganiza mwakuya pokhala pafupi ndi dzenje lalikulu nkumalira
pofuna kupha njovu. Njovu idagwera m’dzenjemo pamene idalondola
komwe kumalira chuleyo poganiza kuti yapeza madzi poti
inkakhulupirira kuti pamene chule akulira padayenera kukhala madzi.
Maphunziro
 Ena amatha kuvulala kapena kufa kumene kamba ka zinthu zochita mwangozi
Njovu idaphedwa pamene idapha ana akalitundulu itatsotsola chisa mwangozi.

 Mwana akamwalira kholo limadandaula komanso amawawidwa moyo kwambirir.


Ana akatundulu atafa onse, katundulu wamkazi ankangodandaula nthawi zonse kotero kuti adavomereza zopha njovu yomwe
idapha anawo.

 Ena akakhala pachisoni sakhala ndi nthawi younguza ngati zomwe anzawo akuwauza ndi zabwino
kapena zoipa.
Katundulu anali pachisoni chachikulu mwakuti adalibe nthawi younguza ngati ganizo lampheta loti njovu iphedwe lidali labwino
kapena ayi. Iye adangovomereza basi.

Page 11
Matanthauzo amawu
 Wakutsina khutu ndi mnansi.
Wakuuza nzeru wakukonda ndithu.

Mawu ena ofuna kuwaunika bwino m’nkhaniyi


 Mnzako ndi amene amakuthandiza panthawi yamavuto.
Mpheta idapezeka/idatulukira ndi chithandizo panthawi imene Katundulu anali pamavuto (anali kulira kamba ka imfa ya ana ake).
Panthawi yomweyinso chule adatulukira ndi chithandizo china: nzeru yophera njovu.

 Kudandaula kokhakokha kusiyanitsa abwino ndi oyipa.


Pamene Katundulu ankangodandaula osachitapo chilichonse kwa njovu yomwe idapha ana ake pomwe idasasula chisa, njovu
ikadakhala yoipa ndipo Katunduluyo akadakhala wabwino. Povomereza ganizo la mpheta loti njovu iphedwe, naye Katundulu
adasanduka woipa poti adapha.

Mutu VI: Imfa ya Mbalame


Nkhani mwachidule
Nthawi ina kutagwa chisanu malingana ndi kusintha kwa nyengo, nkhwere zidavutika ndi kuzizira kwa sabata zingapo. Usiku wina
nkhwerezi zidaona psipsiti(kamphanimphani) yemwe akamauluka amaoneka ngati moto ndipo zidagwira psipsitiyo poganiza kuti adali
moto. Nkhwerezi zidagwetsera pansi psipsitiyo nkumukwirira ndi udzu wouma kuti ukolele ziothe koma udzuwo sudakolele. Izo
sizidadziwe kuti psipsitiyo nkachirombo chabe osati moto. Mbalame ina idafika pamalopo nkulangiza nkhwerezo kuti zidali
kungovutika popeza psipsiti kadali kachirombo chabe komwe kadalibe moto. Nkhwere zinazo zidaleka kuuzira motowo koma imodzi
idapitiriza. Pamene mbalameyo idasendera pafupi kuti itsimikizire nkhwereyo kuti moto padalibe, nkhwereyo idapsa mtima ndi kupha
mbalameyo.

Kusanthula nthano yonse


Zomwe zimachititsa kuti nkhwere zikonde mbali ina yankhalango
Mbali yankhalango imeneyi inali yowirira kwambiri.

Khama lankhwere
Zidauzira udzu ngakhale kuti moto sudayake.

Atengambali/ampangankhani
Nkhwere

Page 12
Mbalame

Malo ochitikira nkhani


Mbali ina yankhalango: Malo owirira kwambiri omwe nkhwere zinkakhala komwenso nkhwere
ina idapha mbalame itapsa mtima
Mfundo zazikulu
 Chikhulupiriro chachikulu
 :Nkhwere sizidasiye kuuzira paudzu ngakhale moto sudakolele popeza zidali ndi chikhulupiriro kuti motowo uyaka basi.

 Kusazindikira
Nkhwere sizidazindikire kuti psipsiti kadali kachirombo chabe komwe kamaoneka ngati moto koma kadalibe moto.

 Nkhanza
Nkhwere idapha mbalame pamene mbalame idatsika kuti ikatsimikizire nkhwerezo kuti moto sungayake .

Maphunziro
Kuthandiza kumaphetsa
Mbalame idaphedwa/idafa pamene idasendera pafupi ndi nkhwere kuti ikatsimikizire nkhwerezo kuti moto sungayake popeza psipsiti
kadali kachirombo chabe kamene kakamauluka kamaoneka ngati moto koma kalibe moto.

Mutu VII: Bulu M’chikopa cha Nkhalamu


Nkhani mwachidule
Munthu wina ankagwira ntchito yochapa zovala za anthu. Adali ndi bulu koma sanali kumusamala mwakuti adali wofooka komanso
sankaona bwino. Tsiku lina adatola chikopa chankhalamu wakufa naveka buluyo kuti azioneka ngati nkhalamuwo, azithawidwa ndipo
azikadya mminda mwawanthu. Posakhalitsa bulu uja adanenepa nakhala ndi mphamvu. Tsiku lina buluyu adamva kulira kwa bulu
wamkazi ndipo pamene adayankhira anthu adadziwa kuti sadali nkhalamu koma bulu ndipo adamupha.

Kusanthula nkhani yonse


Maonekedwe abulu
Anali woonda ndi wofooka

Chomwe chidachititsa bulu kukhala ndi maonekedwe otere


Mwiniwake sankamusala komanso sankamupatsa chakudya chokwanira

Page 13
Cholinga cha mwinibulu pomuveka bulu chikopa chankhalamu
Adzioneka ngati nkhalamu, adzithawidwa ndipo adzikadya m’minda mwa anthu kuti anenepe

Chomwe chidaululitsa bulu


Adamva kulira kwa bulu wamkazi pamtunda wautali ndithu ndipo adatengeka nkuyankhira choncho anthu adamuzindikira kuti sinali
nkhalamu.

Atengambali/ampangankhani
.. Bulu
.. Mwinibulu
.. Anthu am’mudzi
.. Bulu wamkazi
Malo ochitikira nkhani
 Ku minda ya anthu: komwe bulu ankapita kukadya zakudya
 M’balani : mwinibulu amamutsekeramo buluyo m’mawa uliwonse pochokera
kokudya zakudya m’minda ya anthu.
Mkhalango : Kumene munthu ankangodziyedera.
Mmudzi : Komwe anthu ankakhala

Mfundo zazikulu
 Kuchenjera: Mwinibulu adali wochenjera. atazindikira kuti akukanika kumpatsa bulu wake
chakudya chokwanira adamuveka chikopa chankhalamu kuti adzikadya m’minda
mwa anthu mosavutikira.
 Chinyengo : Bulu ankanyengezera kukhala nkhalamu.
 Kudzidalira: Mwinibulu ankagwira ntchito yochapa m’makomo mwa anthu nkumalipidwa.
 Nkhanza : Mwinibulu adaganiza mwankhanza pofuna kudyetsera bulu wake mminda mwa anzake.
 Ulesi : Mwinibulu adali waulesi posamufunira bulu wake zakudya mpaka adawonda ndi kufooka.
Maphunziro
 Kubisa chilengedwe ndi kovuta
Bulu adavala chikopa chankhalamu nkumaopseza anthu, nkumadya zakudya zam’minda mwawo koma atamva kulira kwa bulu
wamkazi pamtunda wautali adayankhira ndipo anthu adamuzindikira kuti ndi bulu osati nkhalamu.

 Kuganiza mwakuya kumathandiza


Mwinibulu atazindikira kuti akukanika kumusamala bulu wake mpaka kumaoneka ofoka adatola chikopa chankhalamu wokufa
Page 14
namuveka kuti anthu asamuzindikire, adziopedwa komanso adzikadya zakudya m’minda yawo mpaka buluyo adanenepa nakhala
ndi mphamvu.

 Chinyengo chimakhala ndi mathero


Bulu adanyenga anthu kwanthawi ndithu nkumathawidwa pomaoneka ngati nkhalamu chonsecho atangovala chikopa cha
nkhalamu. Nthawi idakwana, chinyengo chake chonse chidatha ndipo adaululika naphedwa.

.Kusasamala kumawonongetsa zinthu: mwinibulu adaphetsa bulu wake chifukwa cha kusamusamala pomufunira
zakudya.

Mutu VIII: Udani wa Khwangwala ndi Kadzidzi


Nkhani mwachidule
Mbalame zitavutika posowa mfumu zidaganiza zolonga mfumu yatsopano ndipo mwayi udagwera Kadzidzi. Pamene mbalame
zinakangalika ndi chikonzekero chaphwando la ufumu, mbalame yotchedwa Chikhwangwala idadzudzula mbalamezo kamba kosankha
kadzidzi yemwe adalibe maonekedwe abwino pamene padali mbalame zina zomwe zidali ndi maonekedwe abwino komanso zanzeru
monga Tambala, Kakowa ndi Chiombankhanga. Alangizi adaimitsa phwando ndipo mbalame zonse zidapita kukakambirana. Kadzidzi
adakalipira Chikhwangwala zedi atamva zomwe adachita. Chikhwangwala chidadzitsutsa nkukonza zokapepesa kwa Kadzidzi ngakhale
kuti apa nkuti chidani chitayamba mmtima mwa kadzidzi.

Kusanthula nkhani yonse


Chomwe chidachititsa kuti mbalame zisankhe mfumu
Zidalibe kopita ndi milandu yawo zikalakwirana

Mfundo za Chikhwangwala poimitsa zokonzekera ufumu


 Kadzidzi adalibe nzeru ngati mbalame zina monga Tambala, Kakowa ndi Chiombankhanga.
 Kadzidzi adali wosaoneka bwino monga mbalame zatchulidwazi.
 Kadzidzi sankaona masana.

Kupusa kwa mbalame zonse


Zidasiya kukonzekera nkubwerera komwe zimakhala potsata mfundo zansanje za Chikhwangwala.

Kadzidzi adali ndi mphamvu ngakhale asadamudzodze ufumu


Adakalipira Chikhwangwala kamba koyimitsa zokonzekera kumudzodza iye ufumu.

Malo ochitikira nkhani


 Mnyumba: momwe kadzidzi adakhala pampando akudikira zokonzekera kuti zitsirizika kenako

Page 15
akadzodzedwe ufumu
 Kunyumba za mbalame zosiyanasiyana: Mbalame zinkakhalako ndipo zidapitakonso
pambuyo pa zokambira zoimitsa kulonga
Kadzidzi ufumu
Mfundo zazikulu
 Nsanje: Chikhwangwala adachita nsanje ndi kusankhidwa kwa Kadzidzi kuti alongedwe
ufumu.

 Kuganiza bwino: Mbalame zidaganiza bwino kuti zisankhe mfumu popeza zimasowa
woweruza milandu zikalakwirana.

 Kudzichepetsa: Chikhwangwala adadzitsutsa powutsa chidani pakati Kadzidzi ndi iye ndipo
adaganiza zokapepesa.

 Kulemekeza ufulu wamaganizo pachisankho : Chikhwangwala adapatsidwa mwayi


wopereka maganizo ake pa yemwe adasankhidwa kuti alongedwe ufumu ndipo maganizo ake
adalemekezedwa ngakhale kuti adali ndi nsanje chabe.

Maphunziro
 Nsanje sipindula
Chikhwangwala adayimitsa zokonzekera polonga ufumu wa Kadzidzi kamba ka nsanje chabe komabe
adakapepesa atakalipiridwa nkuzindikira kuti adalakwitsa zinthu.

Mutu IX: Njoka ya Pachulu


Nkhani mwachidule
Njoka sinali kusamala ikamayenda makamaka ikampita kukasaka zakudya. Inali kuponda nyerere mwakuti
zinali kungodzifera. Tsiku lina njoka idadzera njira yaminga ndi miyala ndipo idakhulika komanso idabayidwa
ndi minga komanso miyala ija. Chifukwa cha ululu ndi kuchuluka kwa mabala aminga ndi miyala, njoka ija
idafa ndipo nyerere zidabwera kudzaguza njoka. Nyerere zidapeza mpata wolipsira nkhanza zomwe njoka
inali kuchita.

Kusanthula nkhani yonse


Malo ochitikira nkhani
Page 16
a) Pachulu: malo amene njoka inkakhala
b) Mumkwakwalazi
 Wopanda minga ndi miyala: m’mene njoka inkadutsa nthawi zonse pokasaka zakudya
ndipo sinkasamala zoti ikuponda nyerere.

 Waminga ndi miyala: m’mene njoka idadutsamo paulendo womwe sidakafike kamba koti
idakandidwa ndi minga komanso idakhulidwa ndi miyala mpaka
idafa.
Mfundo zazikulu
 Nkhanza: njoka imaponda nyerere mosasamala ikamapita kosaka zakudya

 Kusasamala: njoka idasankha kudzera njira yomwe sinkadutsamo nthawi zonse mwakuti
sidapitirize ulendo wake pamene idakandika ndi minga komanso kukhulika ndi
miyala mpaka kufa.

 Kusunga mangawa: Nyerere zidasunga mangawa pamene njoka inkaziponda ndipo itafa
njokayo izo zidapeza mpata wokalipsira.
Maphunziro
Kuchitira zinthu limodzi nkofunika
Nyerere zidakwanitsa kuguza njoka chifukwa zidali limodzi zonse.

Mutu X: Moyo wa Mkango


Nkhani mwachidule
Makedzana kudali anyamata anayi okondana. Atatu mwa iwo anali ophunzira, mmodzi anali osaphunzira
koma amakhulupirira nzeru zake zachibadwidwe. Tsiku lina anyamatawa adaganiza zokafuna ntchito poona
kuti kumudziko sikikadawathandiza komanso sukulu yawo sikadaoneka yothandiza. Wamkulu mwa onse
adati wosaphunzira uja asapite nawo popeza palibe munthu angachite naye chidwi. Akuyenda m’nkhalango
paulendo wawo, adapeza mkango wakufa ndipo atatu ophunzira aja adagwirizana kuti abwezeretse moyo
wamkangowo pogwiritsa ntchito nzeru zakusukulu. Atabwezeretsa mafupa, minofu ndi magazi,
wosaphunzira uja adawachenjeza kuti mkangowo udzapha onse akangawubwezera moyo. M’modzi mwa
anyamatawo adadzudzula wosaphunzirayo kuti sadali kudziwa kalikonse. Wosaphunzirayu adachokapo
nakakwera mumtengo. M’nyamata wotsiriza atangouzira moyo m’thupi lamkango, mkangowo
udadzambatuka ndipo udadya anyamata onse atatu aja. Utachoka mkangowo, mnyamata wosaphunzira uja

Page 17
adatsika nabwerera kumudzi akulira kamba ka imfa ya anzake aja.

Kusanthula nkhani yonse


Chidachititsa anyamata kuti achoke dera lakwawo
Ankafuna kukapeza ntchito kudera kwina poganiza kuti kumudziko sikukadawathandiza.

M’mene wosaphunzira adabweretsera mkangano pagulu la anzake ophunzira


 Wamkulu pagulupo adati wosaphunzirayu asapite kunja popeza palibe amene angachite naye chidwi
nkumulemba ntchito.
 Wachitatu adati umenewo sudali mkhalidwe wabwino. Iye adakumbutsa anzakewo kuti wosaphunzirayo
ndi mnzawo kuyambira kuchibwana tsono padalibe chifukwa choti atsale. Adawauza anzake enawo kuti
akamakapeza ndalama kuchokera ku malipiro awo azikamugawira mnzawoyo.

Nzeru za mnyamata wosaphunzira


Adazindikira kuti mkango ukabwezeredwa moyo udzadya onse posayang’anira ntchito yabwino yomwe
anyamatawo angachite choncho adalangiza anzakewo kuti mkango ndi chirombo chomwe chilibe zibwana.
Anzakewo atanyozera langizo lakelo iye adawasiya nkukakwera mumtengo. Mkango utalndiranso moyo
udadya anyamata atatu omwe adaupatsa moyowo.

Malo ochitikira nkhani


 M’nkhalango: anyamata aja ali paulendo wokasaka ntchito adapeza mkango wakufa
m’menemu ndipo pamene adagwirizana zobwezeretsa moyo wake
mkangowo udawadya utalandira moyowo.
 Mumtengo: mnyamata wosaphunzira adakweramo poopa kudyedwa ndi mkango
womwe anyamata anzake ankati awubwezeretsere moyo .
 Kumudzi: komwe anyamata anayi okondana aja ankakhala

Mfundo zazikulu
 Chibwana: anyamata ophunzira adaganiza zobwezeretsa moyo wamkango ndipo atatero
mkangowo udawadya onse.
 Tsankho : anyamata ena ophunzira sankafuna kuti mnyamata mzawo wosaphunzira apite
nawo kutauni poganiza kuti palibe munthu yemwe angachite naye chidwi
nkumulemba ntchito kutauniko.

Page 18
 Kugwiritsa ntchito nzeru molakwika: anyamata ophunzira aja adaganiza zobwezeretsa
moyo wamkango osaganizira makhalidwe a
mkango.
 Chikondi: m’modzi mwa anyamata ophunzira aja adalangiza anzake kuti sikunali kwabwino
kuti amusiye mzawoyo paulendowo popeza adakulira naye limodzi. Iye adauza
anzakewo kuti akakapeza ntchito kutauni aliyense adayenera kumuthandiza
kuchokera ku malipiro awo.

Maphunziro
 Maphunziro okha opanda nzeru zachibadwidwe ndi chabe.
Anyamata atatu ophunzira aja adasonyeza kusowa nzeru zachibadwidwe popereka moyo kwa
mkango, chilombo chomwe chidawadya chitangolandira moyowo.

 Chirombo ndi chirombo ndithu, ngakhale mutachichitira zabwino chimabwezera


ndi zoipa.
Mkango udadya anyamata omwe adaupatsanso moyo.

Mutu XI: Njovu isankhidwa Ufumu


Nkhani myonse mwachidule
M’nkhalango ina, Njovu idasankhidwa kukhala mfumu ya nyama zonse. Nthawi ina mudagwa njala
m’nkhalangomo, madzi adaphwera ndipo nyama zidayamba kufa. Mfumu Njovu idatuma njovu zonse kuti
zikafune madzi. Njovu zidapeza madziwo kuvuma kwa nkhalangoyo pamalo otchedwa Nyanjamwezi. Mfumu
Njovu adapita kukamwa madzi komanso kukasamba. Njovu sizidasamale tizilombo tomwe timakhala
m’madzimo tomwe timachititsa kuti Nyanjamwezi iziwoneka ngati paradizo. Tizilomboto tithyoka makosi
ndipo tambiri tinafa. Nyama zomwe zidatsala ku Nyanjamwezi zidapangana kuti ziletse njovu kudzamwa
madzi. Kanyama konga Kalulu kadadzipereka kuti kakayankhula ndi mfumu Njovu ndipo kadapita
nkukachenjeza Njovu kuti ngati sizisintha khalidwe losasamala ndi kupha nyama ku Nyanjamwezi,
padzakhala mavuto. Njovu idapepesa ndipo idalonjeza kuti m’chitidwewo sudzaonekanso.

Kusanthula nkhani yonse


 Chomwe chidachititsa Njovu kuti isankhidwe ufumu
 Njovu idali khalidwe labwino lodziwa kusunga nyama zonse m’deralo.

Page 19
 Chomwe chidachititsa mfumu Njovu kuti itume njovu zonse kunka
kukasaka madzi
 M’nkhalngo mudagwa njala yayikulu.
 Madzi m’madambo,m’mitsinje ndi m’ngalande adaphwera.
 Nyama zazing’ono zidayamba kufa.

 Ulemu wanjovu zomwe zidasaka madzi


 Zitapeza madzi pa Nyanjamwezi, zidathamanga kukauza mfumu Njovu ndipo mfumuyo idali
yoyamba kukamwa madziwo ndi kusamba

 Maonekedwe a Nyanjamwezi
 Imaoneka ngati paradizo kamba tizilombo tam’madzimo tomwe timaoneka mochititsa kaso.
 Vuto lomwe lidadza njovu zitakamwa madzi ku Nyanjamwezi
 Nyama zam’madzi zidathyoledwa makosi ndipo zambiri zidafa.

 Msokhano wanyama zomwe zidapulumuka ku Nyanjamwezi


 Zidakambirana kuti zipeze njira yoletsera njovu kuti zisadzamwenso madzi ku Nyanjamwezi.
 Kanyama kena konga Kalulu koma kokhala m’madzi kadauza nyamazo kuti njovuzo
sizidzabweranso poti mngelo wake adakatsimikizira zankhani yonseyo.
 Kanyama konga Kaluluka kadadzipereka kuti kapita kukayankhula ndi mfumu Njovu.

 Zokambirana za mfumu Njovu ndi Nthumwi ya Nyanjamwezi


 Nthumwi ya Nyanjamwezi, kanyama konga Kalulu, idauza Njovu kuti njovu zidalakwa
povunduwiza madzi a Nyanjamwezi ndikupha zamoyo zambirimbiri.
 Nthumwi ya Nyanjamweziyi idachenjeza njovu kuti padzakhala mavuto aakulu ngati mchitidwewo
ungapitirire.
 Njovu idapepesa ndipo idapempha momwe ikadakapepesera kwa Nyanjamwezi.

Malo ochitikira nkhani


M’khalango
 momwe Njovu idasankhidwa kukhala mfumu kamba ka khalidwe lake labwino lodziwa kusunga
nyama zonse.
Ku Nyanjamwezi:
Page 20
 Komwe kudapezeka madzi ndipo njovu zidapita kukamwa
 Komwe njovu zidaponda ndi kupha nyama zam’madzi
 Komwe mfumu Njovu idapita kukapepesa pa imfa ya nyama zam’madzi

Mfundo zazikulu
 Kudzichepetsa
 Njovu itamva dandaulo lomwe lidabwera ndi nthumwi ya Nyanjamwezi, kuti njovu zidalakwa
povunduwiza madzi a Nyanjamwezi komanso popha nyama zam’madzi, idapepesa ndipo
idalonjeza kuti mchitidwe umenewo sudzachitikanso.
 Kulimba mtima
 Kanyama konga Kalulu kadadzipereka kuti kapita kukayankhula ndi Njovu pamene njovu
zidaponda ndi kupha nyama zam’madzi ku Nyanjamwezi. Kanyamaka kadali kakang’ono koma
sikadaope kupita kunkhalango komwe kudali nyama zazikulu.
 Nkhanza
 Njovu zidavunduwiza madzi a Nyanjamwezi mosasamala ndipo zidapha nyama zam’madzimo
zomwe zimachititsa kuti Nyanjamwezi iziwoneka ngati paradizo.
 Kukhulupirika/Kutumika
 Njovu zonse zidavomera zopita kukasaka madzi m’malo mwa nyama zazing’ono.

 Chikondi
 Njovu zidakasaka madzi mwa nyama zazing’ono zimene, zina mwa izo, zidali zitayamba kale kufa.

Maphunziro
 Khalidwe labwino limapindulitsa
 Njovu idasankhidwa kukhala mfumu kamba ka khalidwe lake labwino lodziwa kusunga nyama
zonse.
 Kulimbamtima ndi kwabwino
 Kanyama konga Kalululu kadalimba mtima n’kupita kukayankhula ndi Njovu ngati nthumwi ya
Nyanjamwezi pamene nyama zam’madzi zidaphedwa ndi njovu. Mfumu Njovu idapepesa ndipo
idalonjeza kuti mchitidwewu supitirira.
 Ndibwino kuwadzudzula ena akachitira zinthu zolakwika
Page 21
 Njovu zitavunduwiza madzi komanso zitaponda ndi kupha nyama zam’madzi ku Nyanjamwezi,
nyama zotsala zidakwiya ndipo zidatuma kanyama konga Kalulu kuti kakadzudzule njovu kuti
zidalakwa poteropo.
 Ena akaferedwa amachoka mantha nachita zinthu molimba mtima.
 Kanyama konga Kalulu kadachoka mantha ndipo kadalimba mtima kuyankhula ndi mfumu Njovu
popeza kadawawidwa mtima ndi imfa ya abale ake, achinansi, ana ndi azimayi.

Mutu XII: Maloto a Munthu Wosauka


Nkhani yonse mwachidule
Tsokalida, mphawi wotheratu, ankakhalira kupempha mtauni ina. Akadaya nakhuta amasunga zokudya
zotsalazo mumtsuko m’nyumba mwake. Tsiku lina ankachita ngati akulota uku akuyang’ana mikute yomwe
adasunga mumtsuko wakewo. Adaziyankhulira kumalotoko kuti kutagwa njala atha kugulitsa mikuteyo
nkupeza ndalama zomwe angagulire mbuzi zazikazi zomwe zingasawane pakutha pa miyezi isanu ndi iwiri.
Adadziyankhuliranso kuti angathe kugulitsa mbuzizo nkugula ng’ombe zingapo zomwe atazigulitsa akadatha
kugula nyama mbidzi ndi abulu ndi golide. Golide akadzagula naye nyumba yomwe ikadamuthandiza
kukwatira mkazi wabwino nkubereka mwana wamamuna. M’malingaliro mwakemo adaona mwanayo
atalumpha kuchoka m’manja mwa amake nakapezeka pafupi ndi abulu ndipo iye adakwiya zedi poona kuti
kuti mkazi wake adatanganidwa ndi zina ndipo adamukankha. Apa adangozindikira kuti wakankha mtsuko
wa mikute uja ndipo mikute yonse idagwera pansi.

Kusanthula nkhani yonse


 Tsokalida analidi mphawi wotheratu
 Amadya chakudya chochita kupempha.
 Zakudya zotsala amasunga mumtsuko womwe amamangirira kutsindwi la nyumba yake.

 Tsokalida anali wosakwatira


 M’maloto ake adafotokoza kuti akadagula nyumba yomwe ikadamuthandiza kukwatira mkazi
wabwino.

Malo ochitikira nkhani


 Mtauni
 Momwe Tsokalida anali kukhala ndipo anali kupempha zakudya.

Page 22
 M’nyumba mwa Tsokalida
 Momwe Tsokalida ankasunga mikute yake mumtsuko womwe amamangirira kutsindwi.

Mfundo zazikulu
 Kusamala zinthu
 Tsokalida akakhuta, amasunga mikute yotsala mumtsuko.

 Ulesi
 Tsokalida ankangopempha mtauni m’malo mopeza ntchito kwa anthu omwe amampatsa zakudyawo.

Maphunziro
 Nthawi zina maloto ndi woyipa
 Tsokalida adalota akukhankha mkazi wake yemwe adatanganidwa ndi zinthu zina m’malo mosamala
mwana wake, mwakuti adazindikira kuti wamenya mtsuko womwe amasunga mikute yake ndipo
mikuteyo idamugwera.

Mutu XIII:Nkhandwe Yobiliwira


Nkhani yonse mwachidule
Nkhandwe yomwe inkhala kuphanga, tsiku lina ikusaka zakudya idatulukira pamudzi wina. Agalu adayamba
kuyithamangitsa. Nkhandweyo idakabisala m’nyumba ina momwe mudali mgolo wapenti yobiliwira. Mwini
nyumbayi amagwira ntchito ya zopentapenta. Nkhandweyo idagunda mgolo wapenti yobiliwira uja
mwangozi ndipo penti yense adakhuthukira pathupi lonse la nkhandweyo mwakuti idasintha maonekedwe.
Idatulukira khomo lakuseri kwa nyumbayo ndipo idayenda molunjika kunkhalango komwe imakhala. Nyama
zitaona maonekedwe a nkhandweyo zidadabwa ndipo zidayamba kuthawa posayizindikira. Nkhandwe
idauza nyamazo kuti zisathawe popeza iyo idatumidwa ndi Mlengi kuti idzakhale mfumu yawo popeza
nyamazo zimasowa mfumu. Nkhandwe idalandira ulemu woyenera monga mfumu. Tsiku lina mfumu
Nkhandwe akuusa adamva kulira kwa nkhandwe zinzake ndipo idayankhira. Nyama zija zidazindikira kuti
nyama yobiliwira yomwe inkawalamulira idali nkhandwe chocho zidayithamangitsa ndi kuipha.

Kusanthula nkhani yonse


 Kuchenjera kwa nkhandwe
 Idauza nyama zomwe zimathawa m’nkhalango kamba ka maonekedwe ake obiliwira kuti Mlengi
adayituma kuti idzakhale mfumu yawo popeza zidalibe mfumu.

Page 23
 Kupusa kwa nkhandwe
 Idyankhira itamva kulira kwa nkhandwe zinzake pamene inali kuusa poyiwala kuti idakhala
mfumu itanamiza nyamazo.

 Kupusa kwa nyama m’nkhalango


 Zidalonga nkhandwe ufumu pamene nkhandweyo idanena kuti idatumidwa ndi mlengi m’malo
mofufuza bwinobwino kuti nyamayo idali chani.

Malo ochitikira nkhani


 Kunkhalango
 Komwe Nkhandwe idalongedwa ufumu pamene idanamiza nyama zonse kuti idatumidwa ndi
Mlengi kuti idzalamulire nyamazo
 Komwe kudali phanga lomwe nkhandwe inkakhala

 Pamudzi wina
 Pamene Nkhandwe idatulukira ikunka nisaka zakudya

 M’nyumba ya munthu wopenta


 M’mene Nkhandwe idabisala pothawa agalu amene ankayithamangitsa
 Nkhandwe idagundamo mgolo wapenti wobiliwira yemwe adayikhuthukira nkuyisintha
maonekedwe

Mfundo zazikulu
 Kudzidalira
 Nkhandwe idapita yokha kukafuna zakudya
 Mwini nyumba, yomwe Nkhandwe idabisala ikuthamngitsidwa ndi agalu, ankagwira ntchito
yazopentapenta.

 Kudzithandiza
 Nkhandwe idathawira m’nyumba ya munthu wazopentapenta pofuna kupulumutsa moyo wake.

Page 24
 Chinyengo
 Idauza nyama zomwe zimathawa m’nkhalango kamba ka maonekedwe ake obiliwira kuti Mlengi
adayituma kuti idzakhale mfumu yawo popeza zidalibe mfumu.

Maphunziro
 Ndi kovuta kubisa chilengedwe
 Nkhandwe idanamiza nyama zonse kuti idatumidwa ndi Mlengi kuti idzakhale mfumu pamene
nyama zimayithawa kamba ka maonekedwe ake obiliwira. Ufumu udatheka komabe
Nkhandweyo idaululika kuti ndi nkhandwe pamene idayankhira itamva kulira kwa nkhandwe
zinzake ndipo idaphedwa ndi nyama zija.

 Imfa sithawika
 Nkhandwe inkathawa agalu kuti ipulumutse moyo wake. Izi zidatheka ndithu koma idaphedwa
ndi nyama zinzake m’nkhalango pamene zidazindikira kuti mfumu yawoyi idangosintha
maonekedwe koma ndi Nkhandwe.

 Chinyengo sichikhalitsa:chimawululika
 Nkhandwe idanamiza nyama zonse kuti idatumidwa ndi Mlengi kuti idzakhale mfumu pamene
nyama zimayithawa kamba ka maonekedwe ake obiliwira. Ufumu udatheka komabe
Nkhandweyo idaululika kuti ndi nkhandwe pamene idayankhira itamva kulira kwa nkhandwe
zinzake ndipo idaphedwa ndi nyama zija.

 Matanthauzo amawu
 Mwantambasale; mozemba

Mutu XIV: Moongose


Nkhani yonse mwachidule
Munthu wina wokwatira, wamakhalidwe owopa Mulungu komanso adali ndi mwana m’modzi ankakhala
m’tauni ina. Iye ndi mkazi wake ankalera mwana wachilendo wamtundu wa Moongose yemwe adamutola
kunja kwa nyumba yawo. Mwanayu adachita kutayidwa ndi makolo ake. Mkazi wamunthuyu polera
mwanayu samamukhulupirira popeza amadziwa kuti mtundu wa Moongose udali wamakhalidwe ankhanza

Page 25
moti anali kuopa kuti angadzamumenyere mwana wakeyo. Tsiku lina mayiyu adapita kotunga madzi ndipo
adasiya ana onse awiri m’manja mwa mamuna wake namuuza kuti ateteze mwana wawo kwa Moongose.
Mayiyo atangochoka, mamuna wakeyo adachokanso napita kocheza. Mbuvi idatulukira kuti inkulungize
mwana uja koma Moongose adaipha njokayo natsatira mayiyo kuti akamufotokozere nkhaniyi. Mayi uja
ataona magazi pa Moongose adaganiza kuti wapha mwana wake ndipo adakwiya namponyera mtsuko
Moongose. Moongose adafera pompo. Atafika kunyumba adapeza mwana wake ali bwinobwino pambali
pake pali magazi anjoka yomwe Moongose adapha. Mayiyo adalira kamba kokupha mwana wosalakwa
yemwe adaombola mwana wawo ku imfa.

Kusanthula nkhani yonse


 Maganizo aanthu pa mtundu wa Moongose
 Udali mtundu wamakhalidwe ankhanza

 Kutsimikizira kuti Moongose adali mwana watsoka


 Makolo ake adamutaya
 Ankaleredwa mosakhulupiridwa ndi anthu omwe adamutola
 Adaphedwa ndi mayi am’nyumba kamba koganiziridwa kuti adapha mwana wawo pamene
adatsatira mayiyo magazi ali m’manja.

 Moongose adali wachikondi


 Ankasalidwa ndipo ankakayikiridwa ndi mayi wam’nyumba momwe ankaleredwa koma
adapulumutsa mwana wam’nyumbamo pamene njoka ya Mbuvi inkafuna kumuzengereza.

 Mkazi wamamuna woopa Mulungu


 Mayi watsankho yemwe sankakhulupirirra Moongose kamba ka mtundu wakwawo.
 Ankangokhulupirira kuti Moongose ndi wankhanza pamene analibe umboni weniweni.
 Ankamukonda mwana wake mwakuti anali kumuteteza kwambiri.

 Kufanana kwa mtundu wa Moongose ndi mkazi wamamuna


woopa Mulungu

 Onse adali ankhanza:


 mtundu wa Moongose udali wamakhalidwe ankhanza

Page 26
 mkazi wamunthu owopa Mulungu adali wankhanza popeza adapha Moongose
pongomuganizira kuti adapha mwana wake asadafufuze mokwanira.

Malo ochitikira nkhani


 Mtauni ina
 Momwe munthu wina wokwatira, wamakhalidwe owopa Mulungu komanso adali ndi mwana
m’modzi ankakhala.
 Kocheza
 Komwe mamuna woopa Mulungu adapita m’malo mosamala mwana mkazi wake atamupempha
kuti atero iye atapita kotunga madzi.
 Panjira
 Pamene Moongose adafera ataponyeredwa mtsuko wamadzi pamene mayi amwana amene iye
adamuteteza ku njoka ya Mbuvi adamuona ali ndi magazi ndipo adaganiza kuti Moongoseyo
adapha mwana wawoyo.

Mfundo zazikulu
 Mantha
 Mkazi wamunthu owopa Mulungu ankangoopa kuti Moongose akadatha kumenya mwana wawo
pamene sizidali chomwecho.
 Kusasamala
 Makolo a Moongose adamutaya ali wamng’ono
 Munthu wowopa Mulungu sadasamale mwana wake pamene mkazi wake adamusiyira udindo
womusamala iye (mkaziyo) atapita kotunga madzi.
 Kuganiza molakwika
 Mkazi wamunthu woopa Mulungu ankaganiza molakwika kuti Moongose adali wankhanza kamba
kakuti mtundu wakwawo udalinso wankhanza. Izi zidachtitsa kuti aphe Moongose pamene
adamuona ndi magazi pongoganiza kuti adawaphera mwana.
 Kuteteza
 Moongose adateteza mwana wa munthu woopa Mulungu kunjoka ya mbuvi yomwe
ikadamuzengereza.
 Mkazi wamunthu woopa Mulungu adamusiya mwana wake m’manja mwa bamboo ake kuti
amuyang’anire pamene iye ankapita kotunga madzi. Iye ankakayikira Moongose kuti akadatha
kumenya mwana wakeyo.

Page 27
 Kudalira
 Mkazi wamunthu woopa Mulungu adadalira mamuna wake kuti amusamalira mwawo pamene
iye adapita kukatunga madzi.
 Nkhanza
 Makolo a Moongose admutaya adakali mwana
 Mayi wamunthu woopa Mulungu adapha Moongose pongomuganizira kuti adapha mwana wake
kamba kakuti adali ndi magazi chonsecho Moongose adapha njoka yomwe ikadavulaza mwana
wake.

Maphunziro
 Ndibwino kufufuza nkhani tisanapereke chilango
 Mayi wamunthu woopa Mulungu adapha Moongose pongomuganizira kuti adapha mwana wake
kamba kakuti adali ndi magazi. Pamene adathamangira kunyumba adapeza kuti mwana wakeyo
ali bwinobwino popanda vuto lililonse.

 Ena amalangidwa kamba koganiziridwa zolakwika ngakhale


atachita zinthu zabwino
 Moongose adaphedwa kamba koti mayi yemwe ankamusunga adamuganizira kuti adapha
mwana popeza adali ndi magazi m’manja chonsecho magaziwo adali anjoka yomwe inkafuna
kuzengereza mwanayo ndipo Moongose adayipha.

Mutu XV: Chiweruzo cha Vumbwe


Nkhani yonse mwachidule
Pusi ndi Gonando adali pa ubwenzi ndipo ankakhala malo oyandikana kwambiri. Tsiku lina Pusi atachoka ndi
anzake ena kukafuna zakudya nakhala nthawi asadatulukire, Changa adabwera nkudzalowa m’nyumba ya
Pusi popanda chilolezo. Changa adapeza malowa pamene ankathawa anthu osaka. Gonando adada nkhawa
naganiza kuti Pusi wajiwa pamene Pusiyo sanali kubwera kunyumbako. Gonando atapita kukafuna zakudya
tsiku lina, pobwera adapeza Changa atalowa m’nyumba mwake ndipo atamufunsa Changayo adayankha
kuti nyumbayo idali yake popeza sadapezemo munthu monga mwa lamulo kuti ngati wina achoka
panyumba pake kwa masiku angapo wina akalowa imakhala yake. Pusi adalangiza awiriwa kuti apite kwa
Vumbwe poti ankadziwa kuweluza milandu. M’malo moweluza mlandu wa awiriwa, Vumbwe adawapha
nawadya.
Kusanthula nkhani yonse
Page 28
 Ubwenzi wa Pusi ndi Gonondo
 Ankadyera limodzi.
 Ankakhala moyandikana.
 Ankayenderana.

 Kuyipa mtima kwa Changa


 Adalowa nyumba ya Pusi mwini wake kulibe komanso popanda chilolezo.
 Adalanda malo a Gonondo ponena kuti nyumbayo idali yake popeza sadapezemo aliyense.

 Zochitika za Pusi
 Kukomedwa ndi maulendo kukabwera anzake
 Akachoka pakhomo amakhala masiku angapo asanabwere

 Changa ndi Gonondo anali opusa


 Vumbwe atakoloweka chikhatho chake paphewa la Gonondo komanso atayadzamira mano ake
angowe m’khosi mwa Changa, nyama ziwirizi zidaganiza kuti Vumbwe akufuna azimvetsetsa iwo
izo zikamafotokoza nkhani yawo chonsecho Vumbwe ankakonzekera kupha nyama ziwirizi.

Malo ochitikira nkhani


 Kunyumba kwa Pusi ndi Gonando
 Komwe Pusi ndi Gonondo ankakhala nkumayenderana komanso kudyera pamodzi
 Komwe Gonondo adakangana ndi Changa, Changa atalowa mnyumba mwa Gonondo nkumati
ndi yake popeza sadapezemo munthu aliyense.

 Kunyumba kwa Vumbwe


 Komwe Changa ndi Gonondo adapita kuti Vumbwe akaweruze mlandu wawo pamene Changa
adalanda nyumba ya Gonondo

 Kosaka zakudya
 Komwe Pusi adapita ndi anzake ndipo adatha masiku angapo asadabwerere pakhomo mpaka
Changa adalowa nkulanda nyumba ya Pusi

Mfundo zazikulu
Page 29
 Kuba
 Changa adaba nyumba ya Pusi komanso ya Gonondo.

 Nkhanza
 Changa adaba nyumba ya Pusi komanso ya Gonondo ponena kuti ndi yake popeza sadapezemo
munthu aliyense monga mwa lamulo.

 Kupusa
 Gonondo ndi Pusi adali opusa chifukwa Vumbwe atakoloweka chikhatho chake paphewa la
Gonondo komanso atayadzamira mano ake angowe m’khosi mwa Changa, nyama ziwirizi
zidaganiza kuti Vumbwe akufuna azimvetsetsa iwo izo zikamafotokoza nkhani yawo chonsecho
Vumbwe ankakonzekera kupha nyama ziwirizi.

 Kudalira
 Gonondo ndi Changa adadalira Vumbwe kuti aweruza mlandu wawo.

 Malamulo oyipa
 M’nkhalangomu mudali lamulo loti munthu akasowa malo napeza nyumba mopanda munthu
aliyense, atha kolowa m’nyumbayo nkuyisandutsa yake.

 Chikondi
 Gonondo ataona kuti papita masiku koma Pusi sakubwera adapita kukaona kunyumba kwa
Pusiyo.

Maphunziro
 Ena amagwiritsa ntchito malamulo olakwika polanda zinthu
za eni.
 Changa adalanda nyumba ya Pusi komanso ya Gonondo ponena kuti ndi yake popeza
sadapezemo munthu aliyense monga mwa lamulo loti munthu akasowa malo napeza nyumba
yopanda munthu aliyense, atha kolowa m’nyumbayo nkuyisandutsa yake.

Page 30
Mutu XVI: Mnyamata Wolowerera
Nkhani yonse mwachidule
Mu mzinda wina mutagwa njala, zomoyo zambiri kuphatikizapo agalu adasamukamo. Kanjipiti adachoka mu
mzindawu pothawa njalayo nalowerera kudziko lakutali. Kanjipiti adafika pakhomo pa mayi wina amene
sankasamala zakudya; amangoziyika poyera. Kanjipitiyu akalowa m’nyumbamo amadya zakudya zonse
zomwe wazipeza. Tsiku lina atachitanso zimenezi Kanjipiti adamenyedwa ndi anzake panja pa nyumbayo
mwakuti anali ndi mabala thupi lonse. Kumenyedwaku kudachititsa Kanjipiti kudandaula kuti kudali
kwabwino akadakhala kwawo kusiyana ndi kwa eniku. Kanjipiti adabwerera kwawo ndipo anzake
atamufunsa momwe zimakhalira kudziko linalo, iye adangowayankha kuti anthu amadya, akazi amakhala
balalabalala mtauni ndipo mafumu ndi akuluakulu amakhala modzilemekeza namalandira ulemu.

Kusanthula nkhani yonse


 Zotsatira za njala mumzinda
 Zamoyo zambiri kuphatikiza agalu adathawira kudziko lakutali.
 Kanjipiti adathawira kudziko lina.

 Mphotho ya kusapempha zinthu za eni


 Kanjipiti adakunthidwa ndi anthu panyumba ya mayi wina.

 Ubwino wa kwawo munthu wina aliyense


 Aliyense amakhala mwamtendere

 Zomwe anthu amamufunsa mnzawo akamachokera


kuchilendo
 M’mene kudzikolo kulili
 M’mene anthu akumeneko amakhalira
 Zomwe anthu akumeneko amadya
 Zomwe anthu akumeneko amakonda

Malo ochitikira nkhani


 Mu mzinda
 Momwe mudagwa njala ndipo zamoyo zambiri kuphatikizapo agalu adathawa

Page 31
 Momwe Kanjipiti adavutika ndi njala

 Kudziko lakutali
 Komwe Kanjipiti adathawira
 Komwe Kanjipiti ankadya zakudya za mayi wina osapempha mpaka tsiku lina anzake
adamukong’ontha

Mfundo zazikulu
 Bodza
 Kanjipiti atabwerera kwawo ndipo anzake atamufunsa momwe zimakhalira kudziko linalo, iye
adangowayankha kuti anthu amadya, akazi amakhala balalabalala mtauni ndipo mafumu ndi
akuluakulu amakhala modzilemekeza namalandira ulemu. Iye adabisa zoti adathawako popeza
anthu anzake adamkong’ontha.
 Nkhanza
 Anzake a Kanjipiti adammenya mpaka kumuvulaza kamba koti adadya zakudya panyumba ya
mayi wina osapempha.

Maphunziro
 Sibwino kungotenga zinthu za eni osapempha
 Kanjipitiyu adalowa m’nyumba ya mayi wina yemwe ankangosiya zakudya osasamala ndipo
adadya zakudya zonse zomwe adazipeza koma sadapemphe. Tsiku lina atachitanso zimenezi
Kanjipiti adamenyedwa ndi anzake panja pa nyumbayo mwakuti anali ndi mabala thupi lonse.

Mutu XVII: Phanga Loyankhula


Nkhani yonse mwachidule
Mkango wotchedwa Nkhalamu unkakhala m’nkhalango yobiriwira ndi yamitengo yosiyanasiyana. Tsiku lina
utamva njala udasakasaka chakudya koma sudachipeze. Kutada, udaganiza zobisala pa phanga lina. Iwo
udaganiza kuti ugwira ndiponso udya nyama imene ingalowe kukagona m’phangamo. Nkhandwe yomwe
imagona idatulukira ndipo idayamba kuyimba nyimbo isadalowe mwachizolowezi, “Phanga, phangawe
mdima usaka ine ndafika!” Palibe adayankha komabe Nkhandweyo sidafooke idayimbabe. Mkango
udaganiza kuti phangalo limayankhula mwini wake akafika ndipo udadzifunsa wokha m’mene zitathere
pamene panthawiyo silimankhula. Mkangoyo udayesa kuti padali pangano pakati pa phangalo ndi
Nkhandwe choncho udaganiza zoyankha kuti mwina ungagwire Nkhandweyo. Mkangowo udabangula

Page 32
mwakuti nyama zomwe zimakhala mozungulira phangalo zidadabwa ndipo zidadabwa. Nkhandwe idadziwa
kuti m’phangamo mudali mdani ndipo idathawa.

Malo ochitikira nkhani


 M’nkhalango pa phanga
 Pamene Nkhadwe inkakhala ndipo tsiku lina itafika idayamba kuyimba moyankhula ndi phangalo
 Pamene Mkango udafika ndikuganiza zogona dzuwa litalowa kutinso udye nyama iliyonse
yomwe ingalowe m’phangamo
Mfundo zazikulu
 Kuchenjera
 Nkhandwe idali yochenjera popeza ikafika paphanga imayamba yayimba molankhula ndi
phanagalo kuti idziwe ngati mwalowa mdani. Izi zidathandiza Nkhandweyo popeza tsiku lina
itayimba, Mkango utalowa m’phangamo, Mkangowo udabangula ndipo Nkhandweyo idathawa.
 Kupusa
 Mkango udaganiza kuti pali pangano pakati pa phanga ndi nkhandwe pamene Nkhandwe idafika
paphangalo nkuyamba kuyimba moyankhula phangalo. Iwo udaganiza zoyankha kuimbako kuti
mwina ungagwire Nkhandweyo koma utabangula, Nkhandweyo idathawa.

 Kuganiza mwakuya
 Mkango utasakasaka zakudya koma osapeza kanthu kwa tsiku lonse, udalowa m’phanga lina
poganiza kuti nyama yomwe ingabwere kudzagona m’phangamo uyidye.
 Nkhandwe itafika paphanga n’kuyimba koma popanda yemwe adayankhirako nyimbo yake,
udayankhula ndi phangalo kuti ngati siliyankha iyo ibwerera. Mkango womwe umayembekezera
kuti ugwire Nkhandweyo udayankhira nyimboyi mwakuti nyama zomwe zimakhala mozungulira
phangalo zidachita mantha.

Maphunziro
 Nthawi zina tsoka likatsata wina silitha
 Mkango udasakasaka chakudya tsiku lonse koma osachipeza. Utafika paphanga udalowa
poganiza kuti udya nyama yomwe ingalowe m’phangamo koma Nkhandwe yomwe imakhala
m’phangamo itabwera idayimba nyimbo moyankhula ndi phangalo ndipo pamene Mkango
udayankhira nyimboyo, Nkhandwe idadziwa kuti mwalowa mdani choncho idathawa.

Page 33
Mutu XVIII: Msilikali Woumba Mbiya
Nkhani yonse mwachidule
M’misiri wina woumba mbiya adalinso chidakwa. Akatsiriza ntchito yake amapita kumowa. Tsiku lina
ataledzera adaphunthwa nagwa nkutemeka pamphumi. Kuchipatala sadamusamale moyenera choncho
pamphumipo padatsala chipsera(chibambi)choonetsa kuti munthuyo adavulala kwambiri. Patapita nthawi,
m’dzikomo mudagwa njala ndipo atapita kutali adakalowa ntchito ya ulonda. Mfumu yakumeneko pomuona
ndi chipseracho idayesa kuti adali katswiri pankhondo chonsecho chipseracho chidali chabala lomwe lidadza
kamba ka kuledzera. Mfumuyo idamukweza udindo woumba mbiyayu mwakuti adapatsidwa ulemu ndi
mphatso zomwe katswiri wankhondo amalandira kotero kuti anzake ankamuchitira nsanje. Poyendera perete
tsiku lina komanso pofuna kudziwa zomwe msilikali aliyense adachitapo kuti akhale katsiwiri wankondo
komanso nkhondo zomwe adamenyapo, mfumuyo idazindikira kuti munthuyu sadali msilikali. Iye adanena
mwachilungamo kuti adali woumba mbiya ndiponso kuti chibambi chomwe chidali pamphumi pake chidadza
kamba ka ngozi. Mfumuyo idalamula kuti alangidwe koma idasintha maganizo ndikumupempha kuti athawe
anzake asadazindikire kuti iye sadali msilikiali popeza akadamupha. Ngakhale iye adapempha mfumuyo kuti
amulole apite kunkhondo kuti akaonetse luso lake, mfumuyo idakana ponena kuti munthu amene
sadaphunzirepo zankhondo sangapite kunkhondo mpaka ataphunzira zankhondozo.

Kusanthula nkhani yonse


Makhalidwe a woumba mbiya
 Kukonda kumwa mowa
 Kudzidalira
 Kudalira
 Chilungamo
Malo ochitikira nkhani
 Kumudzi wina: komwe kumakhala m’misiri woumba mbiya
 Kudiko lakutali:komwe adapita msilikali woumba mbiya kwawo kutagwa njala
ndipo adalowa ntchito yaulonda
 Kukampu: komwe woumba mbiya adathamangitsidwa ndi mfumu pomupulumutsa
kwa asilikali anzake
Mfundo zazikulu

Page 34
 Chilungamo: Woumba mbiya adauza mfumu mwachilungamo kuti iye sadali msilikali
ndipo sadamenyepo nkhondo ina iliyonse. Iye ntchito yake idali youmba
mbiya ndipo chipsera chomwe adali nacho (chomwe chidakopa mfumu
nampatsa udindo waukulu) chidadza pamene adagwera mbiyazo.
 Chisoni: Mfumu idamvera chisoni msilikali woumba mbiya pamene adaulula
mwachilungamo kuti iye si msilikali koma woumba mbiya pomuchenjeza kuti
achoke mwansanga pakampupo anthu ena asadamuzindikire kuti simsilikali
popeza akadamupha.
 Kusazindikira: Mfumu sidazindikire kuti munthu amene adapatsidwa ulemu
waukuluyo sadali katswiri wankhondo ayi koma katswiri woumba
mbiya.
 Kudzidalira: M’misiri ankaumba mbiya ndipo m’dzikomo mutagwa njala adapita kutali
komwe adakalowa ntchito yaulonda.
 Kudalira: Woumba mbiya adadalira mfumu yakudziko lakutali yomwe idamulemba
ntchito yaulonda.
 Kusasamala:
 Mfumu sidafufuze mokwanira za woumba mbiya pamene imafuna kumulemba ntchito mpaka
kumupatsa udindo waukulu pakampu ya asilikali pamene iye adalibe zomuyenereza kukhala
paudindowo.
 Ogwira ntchito kuchipatala sadamusamale bwino woumba mbiya mwakuti chipsera chachikulu
chidatsala pamphumi pake chomwe chinkasonyeza kuti adavulala kwambiri.
Maphunziro
 Ntchito iliyonse imakhala ndi zoyenereza zake.
Ntchito yomwe adalowa woumba mbiya idayenera munthu amene adapitapo kunkhondo kapena kuti
adamenyapo nkhondo.
 Ena polemba ntchito safufuza bwino makhalidwe ndi
maluso a anthu.
Mfumu sidafufuze mokwanira za woumba mbiya pamene imafuna kumulemba ntchito mpaka
kumupatsa udindo waukulu pakampu ya asilikali pamene iye adalibe zomuyenereza kukhala
paudindowo.
 Pamavuto munthu sasankha ntchito.
Woumba mbiya adakalowa ntchito yaulonda napatsidwa udindo waukulu pakampu ya asilikali

Page 35
chonsecho iye adali katswiri woumba mbiya.
 Maonekedwe amapusitsa
Mfumu idapereka udindo waukulu komanso waulemu kwa munthu woumba mbiya pamene adaona
chipsera pamphumi pake poganiza kuti adali katswiri pankhondo.

Mutu XIX: Chitosi cha Golide


Nkhani yonse mwachidule
Mumtengo wapaphiri lina munkakhala mbalame yomwe zitosi zake zinali zosakanikirana ndi golide. Mlenje
wina pokapumula pamthunzi pamtengowo adadabwa poona chitosi chagolide chomwe mbalameyo idataya.
Mlenjeyo adayigwira mbalameyo itamuyandikira popeza sidadziwe cholinga chamlenjeyo. Adayisunga
mkachikwatu kazingwe zokhazokha naganiza zokanena kwa mfumu podera nkhawa kuti mwina kuti munthu
wina akadamuona akadakamunenera. Mfumuyo idamulanda mbalameyo ndipo idalamula alonda ake kuti
aziipatsa chakudya ndi madzi. Mlangizi wamfumu adauza mfumuyo kuti padalibe chifukwa chowetera
mbalameyo pamene imachokera kudzira ndipo kuti zomwe amanena mlenjeyo zoti chitosi chake ndi
chagolide n’zabodza komanso n’zopanda umboni. Zidali zosatheka mundowe yambalame kupezeka golide.
Mfumuyo idatsekulira mbalameyo itamva malangizowa ndipo mbalameyo idauluka nkutayira chitosi
chagolide pamalopo. Kuchokera pompo sidaonekenso.
Kusanthula nkhani yonse
Mlenje adali wanzeru
 Adachita chotheka kuti agwire mbalame yomwe inkataya chitosi chagolide.
 Atagwira mbalame adaisunga m’chikwatu chazingwe zokhazokha kuti isathawe.
Mlenje adali wopusa
 Adaganiza zokanena kwamfumu zambalame yachitosi chagolideyo podera nkhawa kuti ena akamuona
nayo akamunenera kwa mfumu. Izi zidachititsa kuti mfumu imulande mbalameyo.
Mfumu idali yanzeru komanso yosamala zinthu
 Itamulanda mlenje mbalame yachitosi chagolide, idalamula alonda ake kuti ayisamale mbalameyo
poyipatsa zakudya komanso madzi akumwa.
Mfumu idali yopusa
 Idamvera zomwe mlangizi wake adayiuza kuti padalibe chifukwa chowetera mbalameyo pamene
imachokera kudzira ndipo kuti zomwe amanena mlenjeyo zoti chitosi chake ndi chagolide n’zabodza
komanso n’zopanda umboni. Zidali zosatheka mundowe yambalame kupezeka golide.
 Idatsekulira ndi kupulumutsa mbalame yomwe imataya chitosi chagolide pongomvera malangizo
kuchokera kwa mlangizi wake.

Page 36
Malo ochitikira nkhani
 Pamtengo: Pamene mlenje adapita kukapumula, adagwira mbalame yomwe inali ndi
chitosi chagolide komanso pamene mbalameyi inkakhala
 Kwamfumu
 komwe mlenje adapita kukanena zambalame yachitosi chagolide ndipo mfumu idamulanda
mbalameyo
 Kumenenso mbalame idapulumukira pamene mfumu idatsekulira mbalameyo pamene
mlangizi wake adauza mfumuyo kuti mbalame singakhale ndi chitosi chagolide popeza
imachokera kudzira
M’chikwatu: m’mene mlenje adasunga mbalame yachitosi chagolide kuti isathawe
Mfundo zazikulu
 Kuganiza molakwika komanso mopepera
 Mfumu idamvera zomwe mlangizi wake adayiuza kuti padalibe chifukwa chowetera mbalameyo
pamene imachokera kudzira ndipo kuti zomwe amanena mlenjeyo zoti chitosi chake ndi chagolide
n’zabodza komanso n’zopanda umboni. Zidali zosatheka mundowe yambalame kupezeka golide.
 Mfumu idatsekulira ndi kupulumutsa mbalame yomwe imataya chitosi chagolide pongomvera
malangizo kuchokera kwa mlangizi wake.
 Adaganiza zokanena kwamfumu zambalame yachitosi chagolideyo podera nkhawa kuti ena
akamuona nayo akamunenera kwa mfumu. Izi zidachititsa kuti mfumu imulande mbalameyo.
 Kuganiza mwanzeru
 Mfumu itamulanda mlenje mbalame yachitosi chagolide, idalamula alonda ake kuti ayisamale
mbalameyo poyipatsa zakudya komanso madzi akumwa.
 Mlenje adachita chotheka kuti agwire mbalame yomwe inkataya chitosi chagolide.
 Mlenje atagwira mbalame adaisunga m’chikwatu chazingwe zokhazokha kuti isathawe.
 Kutaya mwayi wopezapeza
 Mlenje adalandidwa mbalame yomwe adagwira yekha ndipo akadapindula nayo kamba ka golide
yemwe adali m’chitosi chake. Iye adaganiza zokanena kwa mfumu podera nkhawa kuti wina
akamunenera akamuona nayo. Mfumu idamulanda mbalameyo.
 Mfumu idamvera malangizo olakwika a mlangizi wake kuti padalibe chifukwa chowetera
mbalameyo pamene imachokera kudzira ndipo kuti zomwe amanena mlenjeyo zoti chitosi chake
ndi chagolide n’zabodza komanso n’zopanda umboni. Zidali zosatheka mundowe yambalame
kupezeka golide. Izi zidachititsa mfumu kutsekulira ndi kupulumutsa mbalame yomwe idali ndi
chitosi chagolide yemwe akadapindulira mfumuyo.

Page 37
 Kuchenjera
 Mbalame itangoona kuti yapulumuka idagwetsanso chitosi chagolide kenako idauluka ndipo
kuchokera apo sidaonekenso.

Maphunziro
 Anthu ena amachita zolakwika chifukwa choganizira kapena
kumvera zonena za anthu.
 Mfumu idamvera zomwe mlangizi wake adayiuza kuti padalibe chifukwa chowetera mbalameyo
pamene imachokera kudzira ndipo kuti zomwe amanena mlenjeyo zoti chitosi chake ndi chagolide
n’zabodza komanso n’zopanda umboni. Zidali zosatheka mundowe yambalame kupezeka golide.
Itamva zimenezi idatsekulira mbalameyo ndipo idauluka osadzabweranso.

Mutu XX: Kutha kwa Chikondi


Nkhani yonse mwachidule
Chisesele ndi mzinda wokongola kwambiri womwe unali limwera kwa dziko lina. Njokaipuma, mkulu
wazamalonda komanso wosasowa kanthu, ankakhala mumzindawu. Tsiku lina Njokaipuma adali kuganizira
zachuma. Adaona kuti ndalama sizikwana choncho ziyenera kuonjezekera. Chuma chimafunika chisamaliro.
Kukhala ndi ndalama koma osazigwiritsa ntchito n’chimodzimodzi kungokhala opanda ndalama. Nthawi ina
ali paulendo wopita kutauni pangolo, akudutsa m’nkhalango ina, ng’ombe yake imodzi idalefuka mwakuti
mwendo udatitimira m’matope. Wantchito wake atamuuza za ng’ombeyo yomwe idabwatikizikayo iye
adakhala pamalopo kwa masiku anagapo kudikira kuti ng’ombeyo ipeze bwino. Ng’ombeyo sidapeze bwino
choncho wachumayo adauza wantchito wakeyo kuti adikilire ng’ombe ija mpaka ipeze bwino. M’mawa
wotsatirawo wantchito adatsala ndi ng’ombe uja adatsatira mbuye wake namunamiza kuti ng’ombeyo yafa.
Wachumayo adamva chisoni nachita mwambo wonse wokhudza imfa yang’ombeyo nkupitiriza ulendo wake.
Ng’ombeyo itapeza bwino idatsatira mkukuluzi wamatayala mpaka idakapeza mbuye wakeyo.

Kusanthula nkhani yonse.


Mzinda wa Chisesele
 Mzinda wokongola kwambiri kupambana mizinda ina yonse ya m’dzikomo
Nkhalango ina
 Inali yowirira zedi
 Inali ndi madzi ochuluka komanso udzu

Page 38
 Inali ndi nyama zosiyanasiyana
 Inali yoopsa zedi
Njokaipuma anali olemera kwambiri
 Anali ndi antchito ambiri.
 Adanyamuka nkumapita kutauni pamodzi ndi antchito ake
 Adayenda pangolo paulendo wakutauni
 Anali ndi katundu wambiri paulendowu

Maganizo a Njokaipuma monga munthu wachuma


 Ndalama sizikwana ngakhale zichuluke chotani.
 Ndalama ziyenera kuonjezekera.
 Munthu akakhala ndi chuma, azichisamala chumacho pochigwiritsa ntchito mosamala.
 Kusunga ndalama osazigwiritsa ntchito n’chimodzimodzi kungokhala opanda ndalama.
 Ndalama zigwiritsidwe ntchito kuti zioneke kapena kugulira zinthu zokagulitsa kuti ndalamazo
zizichulukachuluka.

Zomwe zidachititsa kuti ng’ombe imodzi yokoka ngolo ilefuke


 Ngolo idasenza/idanyamula katundu wambiri.

Malo ochitikira nkhani


 Chisesele
 Mzinda wokongola kuposa mizinda ina yonse m’dzikomo momwe Njokaipuma ankakhala.

 M’nkhalango ina
 Nkhalango yowirira ndi yoopsa m’mene wachuma ndi antchito ake adakhalamo podikira kuti
ng’ombe yomwe idalefuka ndi kutitimira m’matope ipeze bwino
 Wantchito wina adatsalamo yekha atalamulidwa ndi Njokaipuma kuti ayang’anire ng’ombe yomwe
idatitimira m’matope ndipo sinkapezabe bwino

Mfundo zazikulu
 Mantha
 Wantchito yemwe adalamulidwa ndi Njokaipuma kuti ayang’anire ng’ombe yodwala pamalo ena
m’nkhalango, adatsatira mkuluyo tsiku lotsatiralo namunamiza kuti ng’ombeyo yafa chonsecho
idakali moyo. Iye adachita izi kamba kamantha popeza m’nkhalangomo munali moopsa.
 Wantchito wa Njokaipuma, yemwe adalamulidwa kuti atsale ayang’anire ng’ombe yodwala

Page 39
mpaka itapeza bwino, adavomera kamba mantha poganizira mawu omwe abwana ake
adayankhula ndipo adanyamuka asadatsirize kuyankhulako.
 Kudalira
 Njokaipuma ankadalira antchito ake. Antchitowa ankaongolera ngolo yomwe amakwera
komanso kusamala ziweto zake monga ng’ombe zokoka ngolo
 Ng’ombe idadalira wantchito wa Njokaipuma yemwe adailondera pamene sinkapezabe bwino
itadikiliridwa kwa masiku angapo pamene idalefuka ndikutitimira m’matope.
 Nkhanza
 Wanthito wa Njokaipuma adaisiya ng’ombe yodwala yokhayokha m’nkhalango yoopsa.
 Njokaipuma adalamula wantchito wake kuti atsale yekhayekha kuti ayang’anire ng’ombe
yodwala m’nkhalango moopsa zedi.

 Chikondi
 Njokaipuma ndi antchito ake adayidikira ng’ombe yodwala kwa masiku angapo m’nkhalango
moopsa kuti ipeze bwino kenako apitirize ulendo wawo.
 Wantchito wa Njokaipuma adalolera kukhala n’kumayang’anira ng’ombe yodwala m’nkhalango
moopsa yekhayekha.
 Ng’ombe yodwala itapeza bwino yokhayokha idalondola mkukuluzi wangolo mpaka idakapeza
mbuye wake ngakhale kuti adayisiya ndi wantchito panjira ndipo wantchitoyonso adayithawa.

 Chinyengo/bodza
 Wantchito wa Njokaipuma yemwe adamusiya kuti ayang’anire ng’ombe yodwala mpaka ipeze
bwino adayisiya ng’ombeyo nakamunamiza bwana wakeyo kuti ng’ombeyo yafa chonsecho inali
idakali moyo.
Maphunziro
 Mantha amachititsa bodza.
 Wantchito wa Njokaipuma yemwe adamusiya kuti ayang’anire ng’ombe yodwala mpaka ipeze
bwino adayisiya ng’ombeyo nakamunamiza bwana wakeyo kuti ng’ombeyo yafa chonsecho inali
idakali moyo. Iye adachita izi popeza ankaopa kukhala m’nkhalangomo yekha.

 Sibwino kungovomera zinthu tikudziwa kuti sitikwanitsa


 Wantchito wa Njokaipuma adavomera zoyang’anira ng’ombe yodwala m’nkhalango moopsa zedi
koma tsiku lotsatiralo adathawa nkuyisiya yokha ng’ombe kamba ka mantha.

Page 40
Mutu XXI: Kwalimba Uta
Nkhani yonse mwachidule
Panali nkhondo yayikulu pakati pa mbalame ndi nyama kamba kolimbirana ufumu. Pena nyama zinkambana
pena mbalame ndizo. Mleme adapezerapo mwayi womakhala mbali yomwe ikupambana kamba ka
maonekedwe ake. Amauza mbalame kuti ndi mbale wawo kamba kakuti ali ndi mapiko. Ndipo akapita kwa
nyama amati ndi mbale wawo kamba kakuti ali ndi manu ndipo thupi lake si lambalame. Mbali zonse ziwiri
zidamtulukira ndipo zidagwirizana kuti zisamlandire konse. Mbalame zidatsindika kuti zikamupeza zimupha
choncho Mleme, kuchokera tsiku limeneli, sayendanso masana kuopa kuphedwa ndi mbalame.

Kusanthula nkhani yonse


Gwero lankhondo pakati pa nyama ndi mbalame
 Nkhondo idabuka kamba kolimbirana ufumu.
Maonekedwe a Mleme
 Anali ndi makupe ngati mbalame.
 Anali thupi laubweya komanso anali manu ngati nyama.
 Amaoneka ngati mbewa.
Nzeru za mbalame pankhondo
 Zidaganiza zomaulukira m’maso mwa nyama nkumakolowola maso komanso kuzozoola.
 Kadzidzi adalimbikitsa nkhondo yausiku popeza saona masana.
Mfundo zazikulu
 Ukathyali
 Mleme anali kupusitsa mbalame ndi nyama pomakhala mbali imene ikuchita bwino(yalimba)
pankhondo yambali ziwirizi. Iye amauza mbalame kuti ndi mbale wawo popeza anali ndi
makupe ndipo nyama kuti ndi mbale wawo poti anali ndi manu.
 Mantha
 Mleme adasiya kuyenda usiku poopa kuphedwa ndi mbalame zomwe zidamukonzera
chiwembu.
 Kuchenjera
 Mleme anali wochenjera popeza amathawira mbali imene yalimba pankhondo.
 Chiwembu
 Mbalame zidagwirizana kuti ziphe Kadzidzi paliponse pamene atamupezepo pamene
zidazindikira kuti ndi mthira kuwiri.

Page 41
 Kudalira
 Mbalame zimadalira Khungubwe, Kakowa, Katema, Nkhuku, Kadzidzi, Chiombankhanga,
Ngoloma, Nang’omba ndi zina pankhani yokolowola maso anyama ndi kuzozoola.
Maphunziro
 Chinyengo chimakhala ndi mathero ndipo chimabweretsa
mavuto
 Mleme ankapusitsa mbalame ndi nyama pamene zinali kumenyanira ufumu pomakhala mbali
imene ikuchita bwino(yalimba) pankhondo yambali ziwirizi. Iye amauza mbalame kuti ndi
mbale wawo popeza anali ndi makupe ndipo nyama kuti ndi mbale wawo poti anali ndi manu.
Mbalame zitamtulukira zidagwirizana kuti zimuphe.
 Vuto lililonse limakhala ndi njira yothetsera
 Mbalame zitagwirizana kuti ziphe mleme, iye adasankha njira yosamayenda masana koma
usiku wokha.
 Matanthauzo amawu
 Kuzozoola: kujompha ndi kuvulaza
 Kukolowola: kuchotsa ndi zala kapena mlomo monga zichitira mabalame

Mutu XXII: Maziko a Chikhalidwe


Nkhani yonse mwachidule
Banja lina ku phiri la Palango linali ndi ana awiri aamuna. Mayi a anawo atapita kukafuna zakudya, mlenje
adabwera naba anawo. M’modzi adampulumuka nathawa ndipo adakaleredwa ndi munthu oopa Mulungu.
Mwana amene adaleredwa ndi mlenjeyu adatengera khalidwe loipa la mlenje ndipo mfumu ina ikudutsa
pakhomopo adauza mbuye wakeyo kuti ayigwire nkuipha. Mwana amene adaleredwa ndi munthu woopa
Mulungu uja adatengera khalidwe la mbuye wake mwakuti ataona mfumu yomwe idathawa mlenje ija
adayiuza kuti yalandiridwa ndipo adayipatsa chakudya ndi madzi akumwa. Adauza mbuye wake kuti
mfumuyo ikhale pamthunzi ndipo ithandizidwe pachabwino chilichonse. Mfumuyo idadabwa ndipo
idafotokoza kuti idakumana ndi mnyamata ngati yemwe adayilandira bwinoyu koma sadayilandire ndipo
amafuna kuyipha. Mnyamatayo adafotokozera mfumuyo kuti mnyamata winayo ndi mbale wake koma
adasiyana maleledwe.

Kusanthula nkhani yonse


Malo ochitikira nkhani
Page 42
 Mbali ya phiri la Palango
 Komwe kunkakhala banja lomwe linali ndi ana awiri aamuna ndipo anawo adabedwa ndi mlenje wina
nakaleredwa mosiyana: wina ndi mlenjeyo, wina ndi munthu woopa Mulungu (pamene adathawa).
 Pakhomo pa mlenje
 Pamene mfumu ina inkadutsa itakwera pabulu ndipo mwana amene adaleredwa ndi mlenjeyo
adauza mbuye wake kuti ayigwire ndikuipha.
 Pakhomo pamunthu woopa Mulungu
 Pamene mfumu ina inkadutsa itakwera pabulu ndipo mnyamata amene adaleredwa ndi munthu
woopa Mulungu adayilandira bwino nayipatsa zakudya ndi madzi akumwa nauza mbuye wake kuti
mfumuyo ikhale pamthunzi ndipo ithandizidwe pa chabwino chilichonse.
Mfundo zazikulu
 Chikondi
 Munthu woopa Mulungu adalera bwino mwana amene adamutola ndipo mwanayo adalandira bwino
mfumu imene inkadutsa itakwera pabulu.
 Kuipa mtima
 Mlenje adaba ana awiri aamuna pamene mayi awo adapita kofuna zakudya. Iye sadalere bwino
m’modzi mwa anawo yemwe sadathawe mwakuti mwanayo ataona mfumu imene inkadutsa
itakwera pabulu, adauza mbuye wakeyo kuti ayigwire komanso ayiphe.
Maphunziro
 Mwana amatengera khalidwe la amene wamulera
 Mwana amene adaleredwa ndi mlenje adatengera khalidwe loyipa la mlenjeyo ndipo adauza mbuye
wake kuti agwire ndikupha mfumu yomwe inkadutsa panyumbapo; pamene mbale wake yemwe
adaleredwa ndi munthu woopa Mulungu adatengera khalidwe labwino lachikondi komanso kusamala
anthu.

Mutu XXIII: Ubale wa Mbewa ndi Njovu


Nkhani yonse mwachidule
Mbewa zinkakhala mosangalala pabwinja lina. Njovu zinkaponda mbewazo popita kukamwa madzi mwakuti
maso ambewazo adathudzuka komanso makosi awo adathyokathyoka. Zina mwambewazo zidafa. Mbewa
zidasonkhana nkukambirana kuti zipeze njira zoletsera njovuzo kuti zikamapita kokamwa madzi
sisamadutsire kubwinjako. Mbewa zina zidatsatira njovu komwe zinkakamwa madziko nkukazipempha kuti
zileke kudzera kumalo komwe zimakha mbewa pamene zikunka kukamwa madzi. mbewa zidauza njovu kuti

Page 43
malowo adali awo kuchokera kumakolo awo choncho zipeze kwina kodzera. Pomva dandaulolo, mkulu
wanjovuzo adakhutira nalonjeza zotsatira langizo la mbewazo. Langizoli siliodatsatidwe popeza popeza
mfumu italamula kuti anthu atchere misampha yokolera njovu, Njovu yoyang’anira njovu zinzake ndi njovu
zina zotsatira zidagwidwa. Zitavutika zidapempha mbewa kuti ziwathandize ndipo mbewa zidabwera
nkudula zingwe zamisamphayo mwakuti njovuzo zidapulumuka.
Kusanthula nkhani yonse
Madandaulo a mbewa
 Zimafa kamba kopondedwa choncho zimapempha njovu kuti zisiye kudzera komwe izo zinkakhala.
Zomwe Njovu zidayenera kuganizira pa madandaulo a mbewa
 Kuchepa sikanthu koma khalidwe
Malo ochitikira nkhani
 Kubwinja
 Komwe Mbewa zinkakhala
 Komwe Njovu zinkadzera popita kokumwa madzi
 Komwe mbewa zidapondedwa ndi kuphedwa
 Komwe njovu yotsogolera ndi zinzake zidagwidwa m’misampha ndipo zidapulumutsidwa ndi
Mbewa
Mfundo zazikulu
 Nkhanza
 Njovu zidaponda komanso zidapha Mbewa paulendo wokamwa madzi.
 Chisoni
 Mbewa zidamvera chisoni Njovu zitakodwa m’misampha yomwe anthu adatchera ndipo
zidazipulumutsa.
 Kuderera
 Njovu zidaderera Mbewa posatsatira pangano loti Njovuzo zisiye kudutsa ku Bwinja popeza
zinkaponda komanso zinkapha Mbewazo.
 Kudalira
 Mfumu idadalira anthu kuti atchere misampha yokolera Njovu.
 Njovu zidsomboledwa ndi Mbewa pamene zidakodwa m’misampha.
Maphunziro
 Kunyalanyaza kumapweteketsa.
Page 44
 Njovu zidanyalanyaza pangano lomwe zidachita ndi Mbewa kuti zisiya kudzera kubwinja
mwakuti zidakodwa m’misampha.
 Vuto lililonse limakhala ndi njira yolithetsera.
 Mbewa zidakachonderera Njovu kuti zisiye kudutsa kubwinja pokamwa madzi popeza
zinkaponda ndiponso zinkapha Mbewazo.
 Mfumu idalamula anthu am’mudzi mwake kuti atchere misampha yokolera Njovu.
 Wina aliyense ndi wofunikira.
 Mbewa zidapulumutsa Njovu pamene zidakodwa m’misampha.

Mutu XXIV: Mwambi wa Kalulu ndi Mkango


Nkhani yonse mwachidule
Mkango wina wolusa komanso wamatama unkapha ndi kudya nyama zosiyanasiyana. Pofuna kuthana ndi
Mkangowu, nyama zidagwirizana nkudandaulira Mkangowo kuti uleke kupha nyama poopa kupezeka
m’mavuto. Nyamazo zidalonjeza kuti zizipereka chakudya kwa Mkangowo malingana usiye kuzipha. Mkango
udavomera ganizolo koma udachenjeza nyama kuti zikapanda kukwaniritsa lonjezolo, udzaphophola nyama
iliyonse mopanda chisoni. Litafika tsiku loti Kalulu akapereke chakudya kwa Mkango, iye adaganize momwe
angaphere Mkangowo. Patsikuli Mkango udakwiya popeza nyama sizidakwaniritse lonjezo lomwe zinachita
ndi Mkango choncho Mkango udaganiza kuti uphe nyama zonse. Kalulu atayandikira pomwe Mkangowo
udagona, Mkangowo udamunyoza kuti anali kanyama kakang’ono, kopanda thanzi komanso kosachititsa
nkhuli ndipo udati umudya nkukadyanso nyama zinzake. Kalulu adauza Mkangowo kuti anzake ena asanu
omwe amabwera kuti adzadyedwe, adadyedwa ndi Mkango wina womwe udati ndi mfumu yankhanlangoyo
osati iwowo. Mkangowo udauza Kalulu kuti awuperekeze kwa Mkango winawo kuti pakaoneke wamphamvu.
Kalulu adalondolera Mkangowo pachitsime pomwe adayika mgwazo. Mkango utafika pachitsimepo udaona
chithunzithunzi chake ndipo udadzigwetsera pamadzipo poyesa kuti ndi Mkango winawo. Udadziponya ndi
mphamvu ndipo udafa kamba ka mgwazo uja. Nyama zidakhalanso mosangalala.
Kusanthula nkhani yonse
Zochitika za Mkango
 Matama
 Nkhanza
 Kuderera
 Kunyoza
Dandaulo la nyama
Page 45
 Mkango umazipha mopanda chisoni nkumazidya
Maganizo anyama pa zochitika za Mkango
 Zithane ndi Mkango
 Ziuze Mkango kuti usiye kupha nyama m’malo mwake nyamazo zizipereka zakudya tsiku lililonse
Malo ochitikira nkhani
 Pachitsime:
 Pamene Kalulu adalondolera Mkango kuti ukakumane ndi mkango womwe Kaluluyo adati udati
ndi mwini deralo ndipo Mkango udadzigwetsera pofuna kupha mkango winawo mpaka udafa
ndi mgwazo womwe adayika Kalulu
 M’dera ina
 Momwe nyama zambiri zinali kukhala ndipo Mkango wina wolusa komanso wamatama
unkapha ndi kudya nyama
Mfundo zazikulu
 Nkhanza
 Mkango unkapha ndi kudya nyama mopanda chisoni tsiku lililonse.
 Kupusa
 Nyama zidalonjeza Mkango kuti ziziwupatsa chakudya tsiku lililonse m’malo moti zidakapeza
njira yophera Mkangowo.
 Kuchenjera
 Kalulu adapeza njira yophera Mkango. Adaunamiza kuti anzake asanu adadyedwa ndi mkango
wina womwe udati ndi mwini deralo. Ndipo adalondolera Mkangowo kuti ukaone mkango
unzakewo. Mkangowo udafa ndi mgwazo womwe Kalulu adayika pachitsime pamene Mkango
udadzigwetsera pamene udaona chithunzi chake chomwe nkuyesa mkango winawo.
 Kulimba mtima
 Kalulu adanamiza Mkango zoti kuli mkango wina woopsa kuposa iwowo ndipo adautsogolera
kuti ukaone mdaniyo.

Maphunziro
 Ena amphamvu ndi oopedwa amagwa/amafa mopusa
kwambiri.
 Mkango unali wamphamvu komanso wolusa koma udamvera bodza la Kalulu kuti kunali

Page 46
mkango wina woopsa. Izi zidachititsa kuti Mkangowo utsatire Kalulu kuti ukathane mdaniyo
mapeto ake udafa ndi mgwazo womwe adatchera Kalulu pachitsime, utaona chithunzi chake
chomwe nkudziponya mwamphamvu poyesa kuti udali mkango winawo.
 Vuto lingakule bwanji, limakhala ndi njira yolithetsera.
 Mkango udasowetsa nyama mtendere koma Kalulu adapeza njira yowuphera.

Mutu XXV: Mbalame ya Kunyanja


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXVI: Mkango ndi Nkhosa


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXVII:Mawu a Bulu


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro
Page 47
Mutu XXVIII:Munthu wa Mulungu
Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXIX:Nsinsonsa ndi Njovu


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXX: Banja la Tambala ndi Nkhwali


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

XXXI: Njovu Yakufa


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Page 48
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXXII: Kusosola Mavu


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXXIII: Owumba Nsalu


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro

Mutu XXXIV: Kam’dothi


Nkhani yonse mwachidule
Kusanthula nkhani yonse
Malo ochitikira nkhani
Mfundo zazikulu
Maphunziro
Page 49
Page 50

You might also like